NKHANI ZA MASEWERO MWATSATANE TSATANE
NKHANI ZA MASEWERO MWATSANE TsATANE
Pamene season ya 2015 TNM super league yatha dzulo, timu Mzuni fc yaonetsa kale khumbo lofuna kudzachita bwino season ya mawa, pomwe timuyi yagwirizana ndi wotsewera wakale wa timu ya flames Russell Mwafulirwa kuti atumikira timuyi chaka cha mawa.
Mzuni siinalekera pompo akuluakulu a timuyi akukambirana ndi m'phunzitsi wakale wa flames a Kinnah Phiri, yemwe waithandizanso timuyi kuti isatuluke mu ligi yayikuruyi kuti akhalebe ndi timu ya Mzuni.
Atapulumuka pomwe anali pa chi opsezo chotuluka mu ligi, timu ya Epac, yaponya maso patsogolo pomwe akuayang'anila osewera angapo kuti alimbitse timu yawo.
Timuyi, ikuyang'anila za katswiri wa Silver Strikers, Ndaziwona Chatsalira yemwe malinga ndi timuyi, chikhulupiliro ali nacho kuti amutenga pomwe makolo ake a katswiriyu atsimikizila timuyi kuti Chatsalira akufuna kuchoka ku timu ya Silver.
Kupatula Chatsalira, timuyi yati ili mkati kukambilana ndi katswiri wa dziko la Zimbabwe yemwe ali kale dziko muno kuti atumikile timuyi.
Kuwonjezela apa, Epac ikhozaso kubweletsa katswiri otchinga ku mbuyo wa dziko la Botswana, ndipo malinga ndi timuyi mayina a akatswiriwa sangatchule pakali pano kuwopa kuyendedwa njomba ndi matimu ena.
Ngakhale anakana kunena za tsogolo lake kutsatila za kutuluka kwa timu yake mu ligi, mphuzitsi wa timu ya Dedza Young Soccer, Miliyasi Pofela Jegwe wavomela kuti timu ya Be Forward Wanderers ikufuna zi ntchito zake.
Itagonja timu yake ndi Epac, Jegwe anakana kunena ngati akhalebe ndi timu ya Dedza kapena ayi, ponena kuti akuyenela kupanga chiganizo chomwe chidzakhala chothandiza kwa iye ngati mphuzitsi komanso banja lake.
Jegwe, anaitengela timu ya Dedza mu ligi yayikulu dziko muno kwa nthawi yoyamba mu mbiri ya mpira m'bomali kukhala ndi timu yosewera ligi yayikulu ndipo anaitsogolera timuyi mu ligiyi kufikila pomwe yakanika kudzisungila malo awo mu ligi.
Ndipo, zinali zachidziwikile kuti ena mwa matimu akuyenela kudyelera maso pa mkuluyu, ndi zomwe yachita timu ya Wanderers pofusa mphuzitsiyu kuti apeleke ma pepala a mbiri yake kuti akuluakulu a timuyi awawone.
Ndipo Jegwe watsimikiza kuti izi zachitika kale zomwe zikutanthauza kuti ngati angakondwe nayo mbiri yake, Pofela akhoza kukakhala othandizana ndi Eliya Kananji.
Izi zinalinkhani zachikopa pamalawi
Munali
Ndiine
JEZ NO 7
Frackson luweya

0 comments