NKHANI Za uku ndI UKU

By Unknown - December 29, 2015

NKHANI Za uku ndI UKU




NIGERIA


Ana 1 Miliyoni a Mdziko la Nigeria ndi Mayiko Atatu Sakupita ku Sukulu 
 
Malipoti a nthambi ya United Nations yoona za chisamaliro cha ana yapeza kuti chiwerengero cha ana 1 miliyoni a mdziko la Nigeria komanso maiko atatu oyandikana ndi dzikolo sakupita ku sukulu kaamba ka gulu la zigawenga za Boko Haram.
Malipoti a wailesi ya BBC ati sukulu zoposera 2 sauzande zinatsekedwa ndipo zina zinasandutsidwa malo okhalamo zigawengazo.
Pulezidenti wa dzikolo Muhammadu Buhari ati anauza asilikali a dzikolo kuti pomafika mapeto a mwezi uno, akhale atathana ndi zigawengazo ngakhale kufikira pano zigawengazo zikuponyabe mabomba mmadera osiyanasiyana mdzikolo.
Malinga ndi malipoti  kufikira pano zigawengazi zapha anthu okwana 17 sauzande ndipo anthu oposera 2 miliyoni akusowa pokhala.
Padakali pano gulu la zigawenga za Boko Haram linafalikira mmaiko a Cameroon, Chad komanso Niger omwe ndi oyandikana ndi dziko la Nigeria.




BURUNDI
Anthu Pafupifupi 50 Afa Mdziko la BurundiAnthu Pafupifupi 50 Afa Mdziko la Burundi 
 
Anthu pafupifupi makumi asanu ndi anayi afa potsatira zipolowe zomwe zinachitika mmadera atatu okhala asilikali  mdziko la Burundi.
Malipoti a wayilesi ya BBC ati mwa anthu omwe aphedwawo matupi a anthu makumi atatu ndi anayi apezeka ali mu nsewu ndipo padakali pano sizikudziwika ngati chiwerengero cha matupi omwe apezeka mu nseuwo chaphatikizidwa ndi chomwe asilikali a dzikolo apeza.
Kusamvana mdziko la Burundi kunayamba pomwe Pulezidenti wa dzikolo Pierre Nkuruzinza analengeza kuti apikisana nao kachitatu pa chisankho cha pulezidenti chomwe chinachitika mdzikolo.
Malinga ndi malipoti anthu 2 hundred and 40 akhala akuphedwa kuyambira mmwezi wa May ndipo 2 hundred sauzande anathawira mmaiko oyandikana nao.




EGyPT

Boma la Dziko la Egypt Alipempha kuti Lipereke Chitetezo ku Mipingo ya Mdzikolo 
 
Mabungwe omenyala ufulu wa anthu mdziko la Egypt apempha boma la dzikolo kuti likhwimitse chitetezo ku mipingo ya  mdzikolo.
Ma bungwewa apereka pempheloli potsatira chiwopsezo chomwe mpingo wa Orthodox walandira kuchokera ku gulu la zauchifwamba la Jihadist.
Gululi ati likukonza zokachita zamtopola pa tchalitchi lina la mpingowu ndipo popereka chiwopsezocho lachita kufotokoza   malo omwe tchalitchilo limapezeka  komanso mmene chinamangidwira.
Padakali pano apolisi mdzikolo ati ayamba kale kuteteza malowo.
Gulu la Jihadist lakhala likupereka chiwopsezo ku magulu osiyanasiyana mdzikolo ndipo mu chaka cha 2011 gululi linachita zamtopola pa tchalitchi lina mdzikolo pomwe   anthu okwana 26 anaphedwa.    



SOUTHAFRICA
Bungwe la SA Medicines Control Council Livomela Mankhwala Othandiza kupewa Kachilombo ka HIV 
 
Bungwe la South Africa Medicines Control Council mdziko la South Africa lavomeleza kuti mankhwala omwe anapangidwa pofuna kupewa kutenga kwa  kachilombo a HIV ayambe kugwira ntchito mdzikomo.

 
Mankhwalawa omwe akuwatchula dzina loti Truvada ndipo ndi ama pilisi akuyenera kumamwedwa tsiku lililonse .
Malipoti  a Nyuzi 24 ati  mankhwalawa athandizanso kuchepetsa chiwerengero    cha achinyamata omwe ndi apakati pazaka 15 komanso 20 kamba koti ndi gulu la anthu omwe ali pachiwopsezo chotenga kachilomboka.
Malinga ndi malipoti mankhwalawa cholinga chake chinali chofuna kuti azichiza   matenda a EDZI   koma atayesedwa, zotsatira  zapezeka kuti   zithandiza munthu amene alibe matendawa      kuti  asatenge   kachilomboka.
Mankhwala asanayambe kuperekedwa mzipatala za mdzikomo ati awona mmene angakhudzire ntchito ya zaumoyo mdzikomo. 
 


AMERiCa
Dziko la America Lithana ndi Zigawenga 
 
M’tsogoleri wa dziko la America a Barack Obama wati dziko la America liyesetsa pothana ndi magulu a zigawenga omwe akulimbikitsa ziwembu m’mayiko  osiyanasiyana.

 

Iye walakhula izi pokhudzidwa ndi imfa ya anthu khumi ndi anayi omwe aphedwa pa chiwembu chomwe magulu ena a zauchifwamba achititira anthu okhala ku San Bernardino m’dzikomo.

 

Iye wati zomwe zachitikazi ndi zokhudza kwambiri choncho mkofunika kuti dziko lake litengepo mbali pa ntchito zowonetsetsa , kuti anthu a m’dzikomo akukhala mwa bata ndi mtendere.

 

Magulu a zigawenga omwe padakali pano ndi amene akusowetsa mtendere m’mayiko osiyanasiyana ndi monga la Islamic State IS lomwe linakachitanso chiwembu ndi kupha anthu oposera zana limodzi mdziko la France  la Boko Haram m’dziko la Nigeria ndinso la  Al Shabaab m’dziko Somalia.

M’tsogoleri wa dziko la America a Barack Obama wati dziko la America liyesetsa pothana ndi magulu a zigawenga omwe akulimbikitsa ziwembu m’mayiko  osiyanasiyana.

 





Munali ndi ine

Frackson luweya

  • Share:

You Might Also Like

0 comments