Abengo anapita kukacheza kwa achibale awo ku tawuni.
Anawapatsa chipinda chogona kumene kunali mabedi awiri. Yawo komanso ya mwana wang'ono.
ENI NYUMBA: Pepanitu Abengo mugona chipinda cha mwana
ABENGO: Palibe vuto pamenepo ndizimukambira nthano
Mkati mwausiku Abengo nkodzo unawapola. Anaganiza zopita panja kukakodza koma amaopapo after atamva kuti kutauni kumayenda anthu odula ziwalo usiku.
Mwachangu anasinthanitsa mabedi aja kumuika mwana pa bedi lawo iwo ndikukodzera la mwana lija kenako kumubwezeretsa mwanayo kuti mamawa adziti mwana wakodza.
Abengo atabwelera pa bedi lawo anapeza kuti mwana uja wabibilapo!
0 comments