Aliyense pamene akuwerenga nkhani yomwe ili yokhudza ndiyosisimutsa amaganiza zolapa Kapena zosintha moyo wake kwa nthawi imeneyo yokha,akamaliza amathadi kulapa koma akachoka malo amenewo nkupita kwina amakasintha maganizo Ndikuti nthawi ilipo ndilapabe,zindikilani kuti pamene mukuti nthawi ilipo ndipamenenso Mumakhala mukuichepesa nthawi yanu,chomwe chimachitika ndichoti mukamawerenga nkhani Ija satana amakhalanso Ali pambalipa kuwerenga nawo ndikukuthandizani mzeru ndiye poti kwa nthawi imeneyo Mumakhala mwakhudzidwa kwambiri amatha kukusiyani mulape,,koma poti Mumakhala mwapemphera mosalimbika iye amadziwanso kuti mukapita kwina akakugonjetsani,
izi zimamuchutikila pafupifupi aliyense motinso zomwe ndalembazi zitha kulapisa wina kenako nkubwereraso kuuchimo!
PHUNZITSO:
Dziwani kuti izi mutha kuzithesa pokha pokha mutakhala mwakakamila mapemphero ndikupemphera muchonadi,
0 comments