­
­

CHIFUKWA CHANI SUMATHOKOZA MULUNGU?

By Unknown - February 17, 2018




CHIFUKWA CHANI SUMATHOKOZA MULUNGU?
Ngat uli pa line tawelenga uthengawu.
Bambo wina wazaka 85 anadwala mwasiliyasi matenda akusowa kwa mpweya. Mwachangu adathamangila naye kuchipatala komwe adakamuika ma paipi opumila kwa 24hrs. Patapita nthawi bambo uja adachila ndipo dokotala adabwela ndi bill yandalama zokwana k200000. Pamene nkuluyo adaona bill yandalamazo iye sadachitile mwina koma kuyamba kulila.
Dokotala adamuuza nkuluyo kuti asalile chifukwa ndalamayo azilipila pang'ono pag'ono. Nkulu uja adamuyang'ana dokotala uja ndipo adati kwa iye.":
Sindikulila chifukwa chakuchuluka kwandalamaz ai olo pompano nditha kukupasani zonse opanda kusala ngongole. chomwe ndikulila ndichakuti mwandiuzila mpweya kwa 24hrs yokha koma ndikulipila k200000. Pamene ndakhala ndikupuma mpweya waulele ochokela kwa Mulungu nthawi yaitali mpaka pano ndili ndizaka 85 opanda kulipila kanthu. ...........
Kod 24hrs mwakhala mukundiuzila mpweyayi kukanakhala kut Mulungu amandilipilisa mpweya wake pazaka zonsezi mukuganiza kuti ndikanakhala ndingongole zochuluka motani?
PHUNZILO
M,bale wanga ukuwelengawe tazifunse wekha pazaka zomwe wakhala ukupuma mpweya wamulungu koma opanda kulipila ngakhale siliver, kod Mulungu akanakhala kut amakulipilisa ukanakhala ndingongole zochuluka bwanji? Kod kukukondela pokupasa moyo nkumapuma mpweya waulele sichifukwa chokwanila choti ukhoza kumuthokozela Mulungu
Tangoyesela kusia kaye zomwe ukupangazo kwa 2secs yokha ndikuthokoza Mulungu polemba AMEN, kuti apitilize kukupyolesa kunsinga zoipa. Mulungu akwezeke ndikutamandika nthawi zonse.
in Jesus Name Amen.

  • Share:

You Might Also Like

0 comments