Tikamawelenga buku lopatulika timamva pamene Yesu Khristu analankhulapo za aneneri onyenga kapena kunena kuti abodza

By Unknown - February 18, 2018


Tikamawelenga buku lopatulika timamva pamene Yesu Khristu analankhulapo za aneneri onyenga kapena kunena kuti abodza . Yesu anati mu nthawi yotsiriza kuzabwera aneneri onyenga ochuluka omwe azanamiza ndikusocheretsa anthu.
...
Yesu ananenetsa kuti aneneriwo azakhala AMBIRI. Komabe ngakhale anatero ananenanso mau ena olimbitsa mtima otsangalatsa, Ambuye Yesu anafotokoza kuti aneneriwo azaziwika ndi zipatso zao.
...
Mtengo uliwonse umabereka chipatso chake, mtengo wamandimu(lemons) ukhoza kunama kuti iwowo ndi wama orange, musalimbane nao, udikireni nthawi yazipatso suzabeleka ma Orange uzabeleka mandimu basi.
...
Mneneri wodzodzedwa komanso woyenda ndi masomphenya a Mulungu sabala chipatso choipa.
Kodi onyengawa tingawadziwe bwanji?
*# AMALALIKIRA KWAMBIRI ZA CHUMA CHA DZIKO LAPANSI MMALO MOTSINDIKA ZA CHIYERO:
Palibe mneneri yemwe anadzodzedwa ndi mphamvu ya kumwamba kuti alalikire kwambiri za chuma cha dziko lapansi mmalo motsindika ulaliki wa chiyero.
AHEBRI 12 VS14 bible likuti KUPANDA CHIYERO PALIBE MUNTHU AKAKUMANE NDI AMBUYE.
Yesu akuti munthu azapindulanji akapeza zonse za dziko lapansi koma nataya moyo osatha.
...
Aneneri omwe amatsindika ma maulaliki awo kwambiri pa zachuma mmalo mochenjeza anthu kuti alape ndikukomzekeretsa anthuwo ku mkwatulo omwe watsala pang'ono kuchitika ndi abodza! Kapena tinene kuti m'busa ameneyo alibe masomphenya a kumwamba. Abale Masomphenya akumwamba ndi akuti munthu akhulupilire Yesu Khristu kuti asatayike koma akakhale nawo moyo osatha (Yohane3 vs16).
...
Pa atumiki onse omwe Mulungu anawadzodza tikawerenga bible ngakhalenso kuphatikiza mwini wake Yesu, uthenga oyamba kuwauza anthu unali oti "LAPANI, chifukwa ufumu wa kumwamba wayandikira!''.
Mtumiki yemwe akukhala busy kumalalikira kuti mulemera, more miracles and wonders ndi zina zokomedwetsa za dzikoli lapansi, mmalo motsindika zoti ulape kuti ukomzekere za kubwera kwachiwiri kwa Yesu, amenewo ndiye abodzao, akhoza kumaliziwa baibulo kukutumula ma verse koma mphamvu yake anaikana.
...
Mateyu 3 vs 2, uthenga oyamba wa Yohane mbatizi unali owachenjeza anthu kuti '' Lapani chifukwa ufumu wa kumwamba wayandikira! Ngakhale Ambuye Yesu sanayambe ndikulalika za ma miracles and wonders, Big No!
Mateyu 4 vs17 bible likuti Yesu atangochoka ku chipululu ndukuyesedwa ndi satana, uthenga oyamba unali oti '' LAPANI chifukwa ufumu wa kumwamba wayandikira
...
Pa Mateyu 10 vesi 7 Yesu akutuma ophumzira ake kuti apite akalalikire. Uthenga oyamba omwe anawapatsa ophumzirawo ndi oti awuze anthu kuti ''UFUMU WA KUMWAMBA WAYANDIKIRA!''
Panali umboni wa busa wina yemwe akuti anaonetsedwa ku gehena. Anafotokoza kuti anawona anthu ku gehena akutemberera azibusa awo. MUkudziwa chifukwa chani amatemberera azibusao? chifukwa sanawachenjeze za mazunzo omwe amakumana nawo ku gehena.
...
Amalalikilidwa za ma miracle and wonders. Ngati lero lino tikukhala bisy kumawalalikira anthu uthenga okoma kuti uwasangalatse osawachenjeza kuti ngati salapa moto ukuwadikira ku gehena, tikuwalakwira, Kuli moto kumwamba wa muyaya!
Mpingo sukapulumutsa munthu koma mpingo umachita kwakukulu kuti munthu ukapulumuke, zilibe kanthu unabadwira momo, kapena makolo ako ndi atsogoleri kapena inu amene muli ndi maudindo koma ngat sizikutheka zachipulumutso, ngati uthenga uwu wakulapa sukulalikiridwa ngati sakunenako zanthawi iyi yachizilizo ndi zoopsa tizakumane nazo ngat sitilapa, kuli bwino kuganiza mofasa gahena its real.

  • Share:

You Might Also Like

0 comments