Tsiku lina kunja kudamdidela ndikuchoka kokasaka chakudya

By Unknown - February 27, 2018



Tsiku lina kunja kudamdidela ndikuchoka kokasaka chakudya kumidzi ina yakutali kudali kosaenela kukafika kunyumba kwanga tsiku lomwelo chifukwa njila yopitila mudzi wakwathu idali yoopsa kwambiri.


Koma chifukwa colikonda banja langa ndidaganiza zozilimbitsa mtima kudusabe mujilayo popangila ana anga ndi mkazi adali asadadye kwa masiku awili.


Ndidayang'ana kumwamba ndi kuti ambuye citani kwaine zomwe mudacita kwa danyeli muja dzenje yamikango.

Ndidanyamuka ulendo opita kumudzi kwathu nditango fika pakati pa nkhalamgo ndidamva kuitana mbuyo mwanga iwe taima pompo nditaceuka ndidaona anthu atatu atanyamula zikwanje manja mwao ndidayamba kuthamangila kusogolo ndidaonanso anthu ena ,4 analinso ndi zida zokutwa kwambiri manja mwao.


Adandizungulila ine pakati ndidangwidwa ndimatha akulu ndikunjenjemela .
Ndidayang'ana kumwamba ndikunena ambuye landilani nzimu wanga komanso musaisiye yokha banja langa
Anthuo adandimgwila ndikundigoneka pansi kuti andizinge kudatulukila cinjoka cacikulu kwambiri yooneka mwacilendo concho yamaso ngati green kuwala kwake kutalika kwake pafupifupi mayadi khumi.



Cidaimika mutu mdikutsegula kukamwa kwake cikunveka phokoso ya ukali komanso njala zigawenga zidayamba kuthawa ine kuti ndizidzuka cidali citafika kale ndidangogona pomwepo cinjoka cidandikwela ndikudusa ndi pamwamba panga mpaka cidatha conse ndikuma thamangitsa zigawengazo ine thawi yomweyo ndidadzuka kuyamba kuthamanga mophuphulika ndidangozindikila ndatulukila manyumba a mudzi mwathu kupulumuka kudatheka.



Kunja kutaca kudamveka kuti munthu wina amezedwa ndi cijoka kunkhalango kuja ndidango dziwilatu kuti ndicimodzi mwa zigawenga zija.
Taonani mulungu zomwe amacita abale ndi alongo amafika pamene nzelu zako zatha.

MPHUNZILO
Tisataye ntima ndi mavuto anthu ayi iye ngokonZeka kutipasa zosowa zathu
komaso kuti pulumutsa
pamavuto ndipamtendere .
Yehova ndi wamakamu iye salemphera .

  • Share:

You Might Also Like

0 comments