Kalekale kunali nkulu wina anakwatira akazi awiri.

By Unknown - March 11, 2018



Kalekale kunali nkulu wina anakwatira akazi awiri.
Nkazi oyamba anali opemphera komanso Okongola koma osabereka.
Nkazi achiwiri anali Oyerekedwa wantudzu koma anamuberekera mwamuna wake ana awiri.
Nkazi wachiwiri nthawi zonse amamunyogodora mzakeyi kamba ka Vuto lake.
...
Koma mwamuna amadzudzula zankhalidweri, ndipo amamuuza nkazi wachiwiriyo Kuti azimulemekeza nkazi woyambayo Chifukwa akadakhala obereka sibwezi iye atamukwatira, ndipo anamuuza uziyamika Mulungu pakusabereka kwake.
...
Nkazi oyamba nthawi zonse amapemphera kwa Mulungu kuti amuchotse chitonzo chosabereka ndipo amupatseko mwana, amapemphera usiku ndiusana.
Patapita nthawi Mulungu anawonetsa ukulu wake ndipo anayima, patapita miyezi 9 anabereka bouncing baby boy.
...
Chimwana chokongola ndipo bambo ake anali kumukonda kwambiri mwana wamwamunayi poti nkazi oyamba uja anangobereka ana akazi okhaokha..MWAON
ANATU CHINSINSI CHAMULUNGU
Nkazi wa chiwiri uyu samamuonera kukondwa mwana wanzakeyu ndipo mzimu oipa unamubwerera kutika amuphe.
...
Tsiku lina nkazi oyamba ndi bambo anapita Ku munda kukalima ndipo anamusiya mwanayo m'manja mwa m'mai nzakeyu poti samaziwa zomwe zili mumtima mwake.
Nkazi wachiwiri yu anangot mwai ndipo anamutenga mwanayi ndikupita naye Ku nkhalango yanjoka zolusa kukamuyika ndicholinga njoka zimuvulaze, abale inu munthu akapita nkhalango imeneyi, sabwerako wa moyo.
...
Makolo atafika kuchokera kumunda anadabwa mwana kulibe ndipo anafusa Nkazi wachiwiryo iye anayankha Kuti anapita kumadzi ndipo nayenso pobwera sanamupeze.
Apa mwini mwana anagwada pansi kupemphera " Ambuye mwana munandipatsa ndinu , chonde ndichitireni chisoni ndizamupezaso Kuti wina "
...
Nthawi imeneyo bambo amwanayi kunali kuyenda nkhomo ndi nkhomo kufunsa ngat aona munthu atatenga mwana koma ai ndithu.
Tsono nkuluyu anafika mpaka kufupi ndi nkhalango yazinjoka ija ndipo anamva kulira kwa Mwana wawo nkhalangomo ndipo bambo analira mofuula Kuti palibe ndi mmodzi yemwe amati akalowa nkhalango iyi amatuluka wa moyo.
...
Koma mai amwana uja analimba ntima kulowa nkhalangomo ndipo anapeza Chinjoka chachikulu Chitamuzinganiza mwanayo ndipo sichikumupanga Chilichonse, Chinjoka Chija Chitawona mmai uja Chinayamba kuzimasura bwino bwino ndikunsiya mwana uja icho ndikusunthapo ndikuima cha potero.
Mai uja atamutenga mwana uja icho chinasowa osaonekanso.
...
Ndipo anapita kunyumba ndichimwemwe. Koma zachison Nkazi wachiwiri uja anamupeza akufuula, anthu atadzadza pakhomo ponsepo, akuti njoka inamuluma pankhomo lolowera Ku Toilet ndipo, anayamba kuulura zonse zomwe anapanga pagulu la anthu mamawa mwake maiyo anamwalira kamba ka ululu wanjoka uja,
...
Baibulo linati okukumbira dzenje adzagwamo okha, inde choipa Chimatsata mwini.
Ngankhale adani atapanga nsanje yotani ngati Mulungu ali nafe Azatimenyera nkhondo,
Mulungu si munthu ndipo palibe angamupangile plan, zosatheka ndi anthu zimatheka ndi iye .
Mulungu akudalitseni nonse #Amen

  • Share:

You Might Also Like

0 comments