M'bale wina zinangofika poti samafunanso kumva

By Unknown - March 15, 2018




M'bale wina zinangofika poti samafunanso kumva izi za Mulungu kapena kuti Jesus Christ, izizi zinali choncho akut kaamba momwe amalingalira moyo wake akanakhala kut Mulungu aliko ndipo amathandiza sakanamulola kut azivutika choncho.
...
Iyeyo amat akamaona ma usinkhu ake, ena njinga zamoto, ma shop, mpaka ena ma lorry 3 tones, iye koma or yopalasa osakhala nao, amati akalingalira samapeza yankho,iyeyo amazit moyo wake ndiwachiwheelbarow ongoyendera kukankhidwa.
...
Tsiku lina ali khale pakhonde maganizo atamukulira, anangoona azimai atatu ndi azibambo awiri afika ma bible awo m'manja..., ndikukhulupira akanawaonera patali akanathawira ndithu...
...
Mwansangala ndi mwachimwemwe anamulonjera, namufunsa ngat analandilapo Yesu anangot zyoliiii osayankha kenako anawayang'ana mosonyeza akuboweka moti anthu anaziwa ndipo anayamba kumutanthauzira mau ena ndi ena zimenenso zinapangisa kut amasuke nanenesa kut sakhulupirira Mulungu kaamba palibe anamuchitirapo.
...
Kagulu kaja kanamufunsa timafunso,
Kodi inu achimwene mene tafika leroli mumoyo wanu mwakagona kangat kuchipatala kut mwadwala... Anayankha sakukumbuka mwina ali mwana....
...
Anamufunsanso..., tikubwera uko tamva galimoto ikulira nseu onse chachitika ndi chani...? Anayankha ndi Ambulance yatenga Maliro ..
Anamufunsanso pakona panseu uwu munthu amakhala pamene paja uja ndiwakut? Anayankha, mukunena olumala komanso osaona uja? Akut eya .... Anayankha kuti kaya, anabwerapo kale kale pamene paja.
...
Kenako kagulu kaja kanati,
eyaaaa zikomo achimwene, mukut mwina muchipatala munagona muli mwana koma tangopitani mukaone lero anthu ali gone gone akusowa moyo ngat wanuwo, galimoto mukut ndi ambulanceyo yatenga Maliro omwalirayo sanafune, akanakhoza kusankha kukhala ndi moyo ngat inu koma sizzinatheke, olumala osaona kwao simukuziwako amagona pomwepo mphepo imeneyi koma inu muli ndi nyumba maso mikono koma mukut simukuziwa chomwe anakuchitirani Mulungu....?
...
M'bale uja anazuka pomwe anakhala kut amvesese, ndipo kagulu kaja sikanasiile pompo anakankhilabe kwakuya namuuza kut, lemekeza Ambuye momwe iwe ulilimo chifukwa alipo ena akusowa zomwe iwe uli nazo, usatengeke ndi ena omwe ali ndi mashop, olemera pakuti sukuziwa njira yomwe anapezera shop yo, sukuziwa utsiku amazuka kangat kuzungulira nyumba, usatengeke ndi awo ali ndi magalimoto sukuziwa ndikatundu wanji akusunga nyumba zao, amene amapembezera usawaone kuchita bwino kunjaku pot zamtendere wawo suziwa, koma mtendere weni weni ndiumene uchoka kwa Ambuye, ukhoza kukhala opanda kanthu koma ulindi mtendere... M'bale ujatu analandila Yesu ndipo pano ndimunthu okhulupirira.
...
Lemekeza Ambuye Momwe ulili. Ambuye azikudalitsani

  • Share:

You Might Also Like

0 comments