NDI NTHAWI YANKHANI ZA MMABOMA,Nkhondo ibuka pakati pa abusa ndi mayi wa udindo Nkhondo ya mundipondera mwana inabuka pakati pa mkazi wa mbusa ndi mai wa udindo mu mpingo wina chifukwa cha nsanje kwa Msakakanya ku Tete mboma la Dedza. Nkhaniyi ikuti mbusa wa mpingowo ndiwa mchiuno ndipo anafunsila mai wina wapa banja yemwenso ali ndi udindo waukulu mu mpingo wakewo. Chibwenzi cha anthu awiriwo
Nkhondo ibuka pakati pa abusa ndi mayi wa udindo
Nkhondo ya mundipondera mwana inabuka pakati pa mkazi wa mbusa ndi mai wa udindo mu mpingo wina chifukwa cha nsanje kwa Msakakanya ku Tete mboma la Dedza.
Nkhaniyi ikuti mbusa wa mpingowo ndiwa mchiuno ndipo anafunsila mai wina wapa banja yemwenso ali ndi udindo waukulu mu mpingo wakewo. Chibwenzi cha anthu awiriwo chimayenda koma sanadziwe kuti akhristu ena anazindikira mpaka anakatsina khutu mkazi wa mbusayo kuti adziwe zomwe zimachitika. Mkazi wa mbusayo sanapupulume ati chifukwa amafuna kuti akhale ndi umboni wokwanila asanakachite za vundu ndipo atatsimikiza anayamba kukonzekera zokabutsa mzakeyo. Tsiku litakwana, mkazi wa mbusayo anavala buluku ndikuyenda molunjika kwa chibwenzi cha mwamuna wakeyo chomwenso ndicha udindo wolozeka mu mpingo wa bamboyo. Atakomanizana, mkazi wa mbusayo sanafunse kanthu chifukwa anafikila kudumphila nzakeyo ndikuyamba kumukanyanga. Wakubayo sanalole chifukwa analimba kwambiri mpaka kuyamba kugubuduzana koma mwini mwamunayo zinali zosadetsa nkhawa chifukwa anavala buluku. Yemwe zinamudera kwambiri ndi mai wakubayo chifukwa anthu woonelera amangogwa ndi phwete kwinaku akumuwowoza malinga ndi zomwe amaona pa nkhondoyo akagwetsana. Panopa, mbusayo ali wela wela chifukwa cha manyazi ndi nkhaniyi.
Afuna kuzembetsa mnyamata wachi albino
Khothi la magistrate mboma la Karonga latumiza ku High Court mlandu wa amuna awiri omwe akuwaganizira kuti amafuna kuzembetsa m’nyamata wachi albino sabata ziwiri zapitazi ncholinga choti akamuphe. Amuna awiriwo Fishani Mtambo wa zaka 35 ndi Wamisi Kaunda wa zaka 32 anakaonekera ku khothi la magistrate-lo lachiwiri lapitali pa mlandu wosunga munthu ncholinga chofuna kumupha. Koma m’khothilo, magistrate Chakaka Nyirenda anati nkofunika kuti mlanduwo upite ku khothi lalikulu. Magistrate Nyirenda anamva kuti mnyamata wachi albinoyo yemwe ndiwa zaka khumi nchimodzi anatsala pang’ono kumupha pomudula mutu koma anthu oyandikira ku maloko anathamanga kukamupulumutsa. Pakadali pano, amuna awiriwo akuyembekezerka kukayankha mlanduwo ku High Court.
Abeledwa ma phone pa maliro
Kwa Mgona mu mzinda wa Lilongwe, mtsikana wina akukhala modandaula kwambiri mnyamata wina atamubela foni zake zam’manja ziwiri atagona pa maliro usiku.
Nkhaniyi ikuti ku deralo kunagwa maliro ndipo anthu ambiri anakagona kusiwako usiku kuphatikizapo mtsikanayo ndi atsinzinamtole omwe. Anthu pa siwapo amacheza molumikizana nkhani bwino bwino koma kenaka aliyense tulo tinampeza mpaka kuyamba kuliza mikonono. Pamenepa ndi pomwe mnyamata wina anaona kuti inali nthawi yake yogwila ntchito ndipo anayamba kudumpha anthu kuchoka komwe anagonako mpaka kukafika pa malo pomwe anagona mtsikanayo malinga nkuti anamuona kale kuti anali ndi mafoni awiri apamwamba. Mtsikanayo pa nthawiyo nkuti atafa nato tulo ndipo mnyamatayo anamusolola mafoni onse awiri ndikuthawa. Podzuka m’mawa, mtsikanayo zinamukoka manja chifukwa akuti anangoti kakasi kusowa poyambila kufunsa komabe anatulukira kuti pali anthu ena omwe sapitila chimodzi ku maliro. Anthu omwe anamva za nkhaniyi anamvera chisoni mtsikanayo ndipo amene anaba fonizo sakudziwika mpaka pano.
Awumbuzidwa kamba koba thumba la flour
Tsinzinamtole wina kwa kabwazi mdera la mfumu Tambala mboma la Dedza waona polekera anthu atamuumbudza chifukwa chopezeka ataba thumba la flour. nkhaniyi ikuti mnyamatayu pamodzi ndi bambo ake amapanga bizinesi yophika tiyi pa masitolo apa Kaname mdera lomwelo. Koma mnyamatayo amachitanso zotolatola mderali. Tsiku lina mnyamatayu analowa mu sitolo ya mkulu wina ndi kuba thumba la flour. Atangoyenda pang’ono anthu anamuona ndikumukwidzinga ndipo kenaka anayamba kumutuwitsa ndi makofi. Pakadali pano nkhope ya mnyamatayu idakali chitupire.
Anjatidwa atagwilira ana awiri
Apolisi mboma la Mzimba akusunga mchitokosi chao Mackbin Phiri wa zaka 23 chifukwa chogwilila ana awili azaka zapakati pa ziwili komanso khumi ndi chimodzi.
Ofalitsa nkhani za apolisi mboma la Mzimba Gabriel Chiona Phiri ankagulitsa zovala pa msika wa Engalaweni ndipo kenaka adaitanitsa atsikana awiliwo koma adakana. Koma atsikanawo atamaliza zogulagula zao adaumba ulendo wopita kwao ndipo Phiri adayamba kutsatila atsikanawo ndipo adawaumiliza kuti agone nao ndipo zitatheka adaugulila atsikanawo botolo la fanta aliyense kuti asakaulule kumudzi. Kufika kunyumba mtsikana wa zaka ziwili adayamba kumva ululu ndipo adayamba kuulula kwa mai ake pa zomwe zidachitika. Kuchiptala zidadziwika kuti atsikana onse awili adawagwilila ndipo adawavulaza komanso kuonjezela apo adawapatsila matenda. Phiri yemwe amachokela pamudzi Muchakache mdela la mfumu Mwirang’ombe mboma la Karonga akuyembekezeka kukaonekela kubwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu ogwilila. Pakadali pano, apolsi mboma la Mzimba alangiza makolo kuti azipewa kutuma ana ao akazi kumsika okha okha.
Afuna kugulisa bwenzi lake lachi albino
Mwamuna wina mboma la Nkhatabay yemwe apolisi adamugwira mboma la Mzimba pomuganizira kuti amafuna kugulitsa bwenzi lake wachi al-bino kwa nzika ina ya dziko la Tanzania wavomera mlanduwo. Phillip Ngulube wa zaka 21, yemwe ndi mphunzitsi pa sukulu ya pulaimale ya Mongo mboma la Mzimba adamugwira Lolemba lapitali pomuganizira kuti amafuna kugulitsa bwenzi lakelo pa mtengo wa 6 million kwacha. M’neneri wa apolisi m’chigawo chakumpoto a Maurice Chapola anati Ngulube akumusunga pa ndende ya Mzuzu podikira chigamulo. Phillip Ngulube amachokera m’mudzi mwa Mtambo, m’dera la Mfumu Timbiri mboma la Nkhatabay.
0 comments