NKHANI zA MASeWeRO AMPIRA
HERE IS MY 2015 TNM SUPER
LEAGUE TEAM OF THE YEAR.
GOAL KEEPER.
1, CHIMWEMWE KUNKAWA.
BULLETS.
He has been voted as the best
goalkeeper at Bullets. As an
analyst stats shows Bullets has
only conceded 24 goals. He must
not be more influential at Bullets
but he has been guiding their goal
post.
2,STANLY SANUDI. WANDERERS.
No doubt he is super league's
best right back. My home based
lad has demonstrated to be
outstanding throughout the
season. No wonder he became the
fan favourite for the Lali Lubani
outfit.
3,YAMIKANI FODYA. BULLETS.
It was obvious the defender would
make in any other analyst team. A
disciplined defender was in a form
of his own. Him and Stanly have
also cemented national team
positions. A HEAD had a sublime
season.
4,CHISOMO MPACHIKA.DEDZA
YOUNG SOCCER. Despite his team
conceding 41 goals but Chiso had
a wonderful season. In his debut
season he managed to become
the hottest player on the Market.
Ability to lead a game with good
interceptions,Chiso can play in
any team, any league.
5,SANKHANI MKANDAWIRE.
BULLETS FC.
I wonder why many pundits are
not remembering him his duties.
The 6ft defender was one of my
best centre half when called. In
the finals of carlsberg against
Wanderers his absence could
clearly seen. He is good both in
air and feet.
6,HASAN ANGANGA CHAPOLA.
MAFCO FC
He must be a big surprise
inclusion to many but for me he is
one of the reason why MAFCO
finished on the second position.
His physicality, accurate and killer
passes plus ability to shoot from
far makes him to have a chance of
finding himself in my fantasy
team.
7, NELSON SILENCER KANGUNJE.
CIVO UNITED.
Let the work of his hands speak
for him. He led an average squad
to win one of the prestigious
trophy with his decisive goals.No
wonder to be christened Silencer.
8,JOHN BANDA. BLUE EAGLES.
Good both at club and national
team. To national team he has
scored vital goals more than
strikers. The Blue Eagles
midfielder was in a form of his
own.
9,CHIUKEPO MSOWOYA. BIG
BULLETS.
He has proven to be the deadliest
striker on the land. He knows how
to hold defenders, creating
chances for himself and
teammates. I like his physicality
and pace.
10,INNOCENT BOKOSI. RED LIONS.
His eight key players teammates
were suspended but nothing
halted him to be the joint top
goalscorer. Helped his team in
shambles while everyone ruled
him out. The Red Lions Striker was
a marvel to watch.
11,KELVIN THOTHO. EPAC FC
Haha he happens to be a good
friend of mine but the former
Dedza Young Soccer excelled well
in left side. His slippery runs
makes him the toughest opponent
to many defenders. He only have
to improve technically and put at a
bay dribbling for the sake of
dribbling like Ox Chamberlain.
Ngakhale inali timu yoyambilira kutsimikizika kuti yalowa mu ligi yayikulu dziko muno kuchoka ku chigawo cha ku m'mwela, bungwe la SULOM, lati mpaka pano sanalandile chikalata kuchoka kwa akuluakulu oyendetsa ligi ya chigawochi kuti Max Bullets ndi yomwe iyimile chigawochi mu ligi.
Izi ndi zosiyana ndi zigawo zina ziwiri, pakati komanso ku mpoto komwe anatsimikiza kuti, Dwangwa United komanso Chilumba Barracks ndi omwe ayimile zigawozi.
Izi, zikutsimikiza zomwe ananena mwini wake wa timuyi, Max Kapanda kuti sakwanitsa kuithandiza timuyi mu ligiyi ndipo ndi okozeka kugulitsa timuyi.
Wa pa mpando wa ligi ya chigawo cha ku m'mwela, Raphael Humba wati akuyenela kukumana ndi mwini wake wa timuyi kuti akambilane kuti chichitike m'chiyani.
Ma bungwe omwe amatengelapo mwayi ndi kutha kwa ligi ndi kukoza mipikisano ing'onoing'ono ya masiku ochepa pakati pa matimu osiyanasiyana , akuyenela kuganizaso kawiri pomwe ena mwa matimu omwe amawadalira anenelatu kuti satenga nawo gawo mu iliyose ya mipikisano yomwe ikozedwe.
Zimakhala za chidziwikile kuti cholinga cha ma bungwewa kumakhala kupeza ndalama zoti agwilitse ntchito pa zolinga zawo, choncho akamatenga matimu amayang'anaso matimu omwe ali ndi chikoka kwa anthu.
Ichi m'chifukwa chake akuyenela kuganizaso kawiri, pomwe matimu awiri omwe ali ndi ochemelera ambiri, Big Bullets komanso Be Forward Wanderers anenelatu kuti osewera awo akufuna apume.
Malinga ndi wa chiwiri wa mlembi ku timu ya Big Bullets, Kelvin Moyo wati apeleka tchuthi kwa osewera awo mpaka mwezi wa Febuluware ndipo ngati atenge gawo ku mpikisano uliwose ndi pa mwambo wa padela okhazikitsa thandizo lawo kuchoka ku kampani ya Nyasa pomwe akuyembekezela matimu a dziko la Tanzania, Zambia komanso Zimbabwe kudzakhala nawo pa mwambowu.
Naye mlembi wa timu ya Be Forward Wanderers Mike Butao wati osewera awo akuyenela kupuma mpaka March.
Ngati njira imodzi yofuna kusintha masewero a mpira kuti apite patsogolo dziko muno, bungwe la Football association of Malawi, laika zoyeneleza za mphuzitsi aliyese yemwe akuphuzitsa timu ya mu ligi yayikulu dziko muno.
Malinga ndi mlembi wa mkulu wa bungweli, Sugzo Nyirenda, akufuna kuwonetsetsa kuti mpira ukupita patsogolo choncho mkoyenela kukhala ndi aphuzitsi omwe ali ndi mapepela okwanila.
Ndipo Nyirenda wati, mphuzitsi aliyese akuyenela kukhala ndi caf B layisesi kuti aphuzitse timu ya mu ligi ndipo akuyembekezela matimu onse kugwilitsa ntchito malamulowa.
Izi zikhudza matimu ngati Be Forward Wanderers, yomwe mphuzitsi wawo Eliya Kananji alibe zomuyeneleza ngati zimenezi.
Bungwe la SULOM, layankhulaso mobweleza, kudziwitsa matimu onse kuti timu kapena osewera yemwe achoke ku timu yake kupita ku timu ina popanda kugwilitsa ntchito njila zoyenela akumana ndi malamuro.
Wakhala m'chitidwe wa matimu a kuno kwathu, kumangotenga osewera ku matimu ena popanda chilorezo kuchoka kwa eni ake osewera zomwe bungweli lati m'chitidwe umenewu sakuwufunaso.
Kuwonjezela apo, bungweli lati akuyenela kudikila pa 14 Januware lomwe ndi tsiku lomwe msika ogula kapena kugulitsa osewera udzatsekulidwe.
Malinga ndi mlembi wa mkulu ku bungweli, Williams Banda aliyese yemwe achite zosemphana ndi malamuro, zilango zidzapelekedwa mosayang'ana nkhope.
Munali ndi ine Jez no7
Frackson luweya

0 comments