Msamuko wa osewera ku timu ya Silver Strikers ukupitilira pomwe timuyi yatsimikiza osewera ena atatu kuti salinso osewera a timuyi. Mbuyomu zinaveka kuti timuyi ikufuna kuchotsa osewera pafupifupi khumi ndipo ngakhale

By Unknown - February 09, 2016

Msamuko wa osewera ku timu ya Silver Strikers ukupitilira pomwe timuyi yatsimikiza osewera ena atatu kuti salinso osewera a timuyi.
Mbuyomu zinaveka kuti timuyi ikufuna kuchotsa osewera pafupifupi khumi ndipo ngakhale akuluakulu a timuyi anakana zikuwoneka kuti izi ndi zoona kamba kakuti osewera akupitilira kuchoka ku timuyi.
Kutsatila kuchoka kwa Green Harawa komanso Ndaziwona Chatsalira omwe anapita dziko la Mozambique komanso Lucky Malata yemwe naye akufuna atakayesa mwayi ku Mozambique , komanso Peter Wadabwa yemwe watengedwa ndi Be Forward Wanderers,
timuyi yalengezaso kuti, Mabvuto Khodzomba, Dailes Yassin komanso Blessings Banda achoka ku timuyi ndipo palinso osewera ena ngati, Ian Banda, John Banda, Peter Pindani, Rodrick Gonani komanso Deco Nyamela akhala akutsatila msamukowu.

  • Share:

You Might Also Like

0 comments