Timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino ya Flames ngakhale yatenga nthawi isanasewere masewero aliwose, yakwela ndi ma sitepe awiri pa ndandanda wa matimu omwe bungwe lomwe limayendetsa masewero pa dziko lonse la FIFA latulutsa
By Unknown - February 09, 2016
Timu ya mpira wa miyendo ya dziko lino ya Flames ngakhale yatenga nthawi isanasewere masewero aliwose, yakwela ndi ma sitepe awiri pa ndandanda wa matimu omwe bungwe lomwe limayendetsa masewero pa dziko lonse la FIFA latulutsa lero.
Timuyi tsopano ili pa nambala 104 pa dziko lonse komanso 28 muno mu Africa pomwe timu yomwe akhale akusewera nayo mwezi wa mawa ya Guinea ili pa nambala 61 pa dziko lonse komanso 10 muno mu Africa.
Timu ya Belgium ndi yomwe ikulamulirabe chikopa pa dziko lonse motsatana ndi Argentina, Spain, Germany ndi Chile.
Muno mu Africa, timu ya Cote d'Ivoire ili patsogolo koma pa dziko lonse ili pa 28, ndipo muno mu Africa ikutsatana ndi Cape Verde Islands komanso Algeria.

0 comments