Timu ya Be Forward Wanderers yatsimikiza kuti zonse zatheka ndipo Peter Wadabwa ndi osewera wa timuyi.
By Unknown - February 09, 2016
Timu ya Be Forward Wanderers yatsimikiza kuti zonse zatheka ndipo Peter Wadabwa ndi osewera wa timuyi.
Watsimikiza izi ndi mlembi wa mkulu wa timuyi Mike Butao yemwe wati ndi okondwa ndi kufika kwa Wadabwa pomwe akufuna kukoza ku tsogolo kwa timu yawo kuti kukhale kwa mphamvu.
Ndipo Butao walonjeza ochemelera timu ya Wanderers kuti sanathele pa Wadabwa koma osewera angapo akhala akubwelaso ku timuyi, Wadabwa ndi osewera wa chitatu kubwela kutsatila Ernest Tambe komanso Rafiq Namwera omwe anawatenga ku Fisd Wizards.
Wadabwa wapita ulere ku Wanderers kamba kakuti analibe kontilakiti ndi timu iliyose ngakhale chaka chathachi amatumikila timu ya Silver Strikers.
0 comments