imu ya Dwangwa United yomwe yabweleraso mu ligi yayikulu dziko muno, yatenga McDonald Mtetemela kuti akhale mphuzitsi wa mkulu wa timuyi. I
Timu ya Dwangwa United yomwe yabweleraso mu ligi yayikulu dziko muno, yatenga McDonald Mtetemela kuti akhale mphuzitsi wa mkulu wa timuyi.
Izi zikudza kutsatila nkhani ya kalabu layisesing'i yomwe mwa zina matimu akuyenela kukhala ndi aphuzitsi omwe ali ndi ma pepala okwanila.
Mtetemela watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati wasayina kontilakiti ya chaka chimodzi ndi timu ya Dwangwa United ndipo wati akudziwa bwino m'mene ligi imakhalira ndipo ntchito agwila.
Dzulo, timu ya Dwangwa United komanso Nyasa Big Bullets akwanitsa ndondomeko yoyambilira ya kalabu layisesing'i ndipo apeleka makalata awo ku bungwe la FAM, zomwe zapangitsa matimu okwanitsa izi kukhala asanu kuphatikizapo Silver Strikers, Red Lions komanso Be Forward Wanderers omwe anakwanitsa kale izi zomwe zikusonyeza kuti matimu a Dwangwa United komanso Nyasa Big Bullets asemphana ndi chilango chomwe chinapelekedwa ndi FAM, kwa matimu omwe sanakwanitse izi.
0 comments