Bambo wina ananyengerera mkaz wokwatiwa yemwe amakhala nae moyandikana mpaka kumagona nae mwamuna wake akapita kuntchito.
By Unknown - February 20, 2018
Bambo wina ananyengerera mkaz wokwatiwa yemwe amakhala nae moyandikana mpaka kumagona nae mwamuna wake akapita kuntchito.
Mwini nkazyu amagwira ntchito yosintha sintha ija ya ma shift, nthawi zina amagwira utsiku nthawi zina masana.
...
Koma nthawi zambiri akakagwira utsiku mamawa pobwera amadabwa zochitika zamkaz wake, ndipo amakaika kut china chake chikuchitika.
Ubwenz wa awiriwo unafumbira moti bamboyo sopano amatha kufika nthawi yabwino kusanade kusiyana ndikale momwe amazembera.
...
Nkulu ogwira utsikuyo anafufuza nkhani yonseyi ndipo anapezadi kuti okondedwa wakeyo amalowesa munthu iye akachoka.
Asanauze aliyense anakakhala pansi ndi mkaz wakeyo nkumufunsa ngt amamudzembera koma mpaka mzimaiyo anaitamitsa baibulo kuti amenye kusonyeza kukana kwambiri kuti sangapange zimenezo pakuti achokera kutali ndipo amamukonda.
...
Atakana motero, nkuluyo sanalekere pompo anakauza abale amkaziyo zonse zingachitike atakhala kuti akumuzembera, mwanjira ina anafuna amulangize ngt m'bale wao, koma zachison namwaliyo anakangowatukwanako abale ake kut asamulowelere pakhomo paopo anachokapo kale, atabwerera komwe amakhala anasambwaza kutukwana ma neba kuti akumuuza mwamuna wake nkhani zaboza.
...
Mwamuna atamva kuti mkaz wake watukwana kwambiri pa linepo, anamva chisoni, ndipo ali kuntchito anauza anzake kuti mkaz wake akumagona ndi munthu, anzake onse anachita kuyang'ang'anizana modabwa ndipo wina anati;
"KODI ZIMENEZI UKUDZIDZIWANSO, IFE TINADZIDZIWA KALE KALE KOMA TIMAOPA KUKUUZA".
Mwini mkaziyo anawauza anzakewo kuti anali kudzidziwa kuchokera kale koma amaganiza asintha amawapasa kae nthawi. Anthu onse aja anamutseka nkumat akufuna AZAGWIRE YEKHA.
...
Angakhale anthu ambiri amamunong'ona mkaz yu ndi relationship yake yambaliyo, komabe sanasinthe amapitilizabe poganiza kut sangazagwidwe, koma tsiku lina nkuluyo anangobwerera kuntchito ndipo anapeza onse ali kuchipinda akucheza ngat banja.
Iye pofuna kulanga kwambiri mwamunayu, anatenga tv, ma speaker ndi zinthu zina zandalama nkuzitulusa panja.
...
Kenako anakuwa kuti kunyumba kwakeko kuli okuba, anthu anathanga ndipo anapeza mwamuna wachilendoyo nyumba mwake ma tv ndi zinthu zina zili panja, nde amati akamufunsa mwamunayu, amati iye siwakuba amabwerera mkaz, pamene mkaz pofuna kuzipulumutsa amakana kut sakumudziwa angofuna populumukira ameneyu ndiwakuba.
Apolice anamutenga nkukamusekera ndipo anaweluzidwa mlandu wakuba napasidwa zaka zake kukakhala kundende.
...
Mkaz ndi bambo aja amaziwa zoona zake, pajatu mkaz anafunsidwa anakana, tsono apapa mwamunayu anangogona osamufunsa mamawa kutacha ananyamuka wakuntchito malinga ndimomwe anapangananila ndi anzake, mkaz yu ataona kuti zathina anangopakila katundu wake nkumapita, analithesa yekha banja anawauza abale ake kut mwamuna sakumufunanso, komatu paja komwe kwagwa mtengo wanthambi sikusowa anthu anadziwa zonse ndipo anamuuza kuti zintchito zake zamusata.
...
Mau amati Mulungu sazalanga munthu asanamudzudzule, abale aja amagonana nkumaona ngat mwini banja sakuziwa koma anali kudziwa ati amawapasa nthawi amawapasa mpata mwina nkulingalira zachoipa amachitacho,,komatu paja amati ukasala pang'ono kufa mumayamba ndi nkutu kugontha.
Ukhoza kumatakata mkaz wanzako, kumaganiza kuti wafasa mwini sakudziwa koma chomwe umaiwala nchoti, ameneyo ndi mkaz wake mwina anadziwa kale akungokupasa mpata, ukhoza kumapanga uhule osaona vuto pomwe anzako ena anaphedwa kuputa matenda ena anamwalira, iweyo sikut wapambana, kapena umadziwa kudzemba koma mwina Mulungu akungokupasa mpata kut uganizire moyo wako zisanaze nthawi zowawitsa.
YONA 1 VS 1...
Yona anafika popakira bag yake ngat akupita ku NENEVI koma nkukakwera SITIMA yaku TALISI, Mulungu akanakhoza kuipanga SITIMA ija osanyamuka kufikira Yona atatsika, akanakhoza kupanga chilichonse pakut palibe chomukanika mpaka Yona asakwere za ku TALISI koma anamusiya kuti mwina alingalire yekha kut akuchita choipa, koma Yona sanalingalire mpaka anakakhala m'mimba mwansomba.
Nkutheka m'bale wakhala ukuchita choipacho mpaka nkumazimva ngat ndiiwe doro, tamvera Mulungu akungokupasa mpata kuti ulape, ukazamva ena akulalika kwambiri zokhuza khalidwe lako loipa usazakalembe pa FACEBOOK nkumat anthu akulondola moyo wako ai, ungoziwa kut ndi Ambuye ameneyo chifukwa iye sazalanga munthu asanamudzudzule. Ukhoza kumatukwana kulemba zonyoza ena matsiku ako nkumapitilira siudolo, ndichikondi chabe ukapanda kuzikkhutula pamaso pake m'bale uzaona ngat Mulungu kulibe, uzaona ngat banja ndilosokoma, uzaona ngat pantchitopo anthu akukuda.
Nthawi zonse onetsetsetsa kuti ukupanga chifuniro chake, utchimo ukazolowereka umaoneka ngat siutchimo koma ukagwidwa ndim'mene umalingalira koma mochedwa BAMBO uja ali kundende MAI uja akuvutika kumudzi.
0 comments