Nditaweluka kuntchito, panjira ndinaona gulu la anthu likuthamangira mbali yakunyumba kwanga. Nditafunsa palibe amaonetsa chidwi chondiyankha. Monga Mmalawi, ndinapinda trauza nkuyamba kulondola.
Zinandidabwitsa kuona anthu onsewo atayima panyumba panga.
Ndiwakhila kuti ndipeze mpata okafika mnyumba. Apolice anandiletsa kulowa koma ndinawauza kuti ndine mwini wanyumbayo.
Nditalowa ndinapeza mwana wanga akuseweletsa chinjoka chachikulu chomwe anthuwo amalephera kuchichotsa mmenemo akazi anga atakomoka chifukwa cha mantha.
Mutu wanga unayima poti panthawiyo chinayamba kumunyambita mwanayo mosonyeza kuti nthawi yiliyonse chikhonza kumumeza.
Mwana wa 2years anakanika kumva kukuwa kwina kulikonse.
Ndipo zimaonetsa kuti chinjokacho chimamusangalasa.
Ndinakumbukira kuti pali kanyimbo komwe kamamusangalatsa ndikayimba.
ndinayamba kuyimba koma mwana sazasuntha. Nkatikati mwanyimboyo munli mau oti bwera mwana wangaaaa! satana ndioyipaaaa! Anthu onse anadabwa mwana atatembenuka.
Ndipo ataona ine anasekelera ndikuyamba kukwawira komwe ndinali.
Ndibamunyamula mwachangu ndikutuluja naye. Apolice anatseka ndikuthira mankhwala mpaka njoka yinafera mommo.
M'bale wanga kodi siukumva mfuwu wa Bambo ako Yehova?
kodi siukudziwa kuti wakhalapo ndipakati pasatana? Ndikudziwa kuti wakomedwa ndikudya zakuba, chigololo, ufiti, kupha, miseche ndi zina zambiri. Imva mfuwu wa Yehova ndikumulondola ndikupeza chipulumutso.
Poti satanayo akukunyengelerandipo akumeza. Choncho tikuyenera kukhala a tcheru mu Thawi ino yotsiliza...
Amen
0 comments