By Unknown - February 25, 2018



Bambo wina nthawi zonse m'mamawa akamapita kuntchito, akafika malo okwerera Bus, amapeza nkulu wina atakhala pa wheel Chair ndipo amatenga kandalama nkumupasa, akatero iye amakwera nkumapita kuntchito.
...
Sindikudziwa kuti zimakhala ndalama zingat koma pafupi fupi daily bamboyo amapeleka kangachepe kwa nkulu owoneka osayendayo.
...
Tsiku lina Bambo uja atafikanso pamalo paja, anakumana ndi zigawenga nkumumenya kumulanda Chilichonse kuphatikiza ndalama ya transport, anasowa chochita m'menemo nkut nkulu wa wheelchair uja alipotero atangofunda buland lake, amaoneka kut sanaonenso zomwe zinachitikazo, angakhale amaona kuti nkulu osayendayo sangamuthandize chilichonse poti ndiopemphetsa, komabe bamboyo anapita namulongosolera zomwe zinachitikazo kwinaku akulingalira kut azibwerera
kunyumba.
...
Atamulongosolera Nkulu osayendayo anamva Chitson kwambiri ndimchitidwe oipa wauchifwamba omwe ukuchitika pamalopo, ndipo anamuuza kut apeze malo okhala adikire pang'ono.
Bamboyu anali odabwa kuti azidikira chiyani, komatu nkulu wapa Wheelchair yo anati;
"INU BAMBO NDI MUNTHU WAMOYO WABWINO, SINDINGALOLE MUVUTIKE INE NDILIPO"
Bambo obeledwayo anangoti kakasi kusowa choyankha pakuti samamvetsa chomwe nkuluyo amatanthauza.
...
Mosakhalitsa anaona Chigalimoto chapamwamba chikufika, mumatuluka driver nkumuyendetsa nkulu wapa wheelchair uja mpaka kukamukweza mugalimoto,anamuuzanso Bambo uja kut akwere.
Bambo uja sanamvetse zomwe zimachitikazo, atafunsa anamulongosolerera kuti, Iye ndi mwini kampani yotchuka ina mutown yo, moti pamene amamupezapo sikut amakhala akupemphetsa koma kudikira driver wake kuzamutenga poti nyumba yake ilikoti sikungafike galimoto.
...
Bambo uja zachiwembu zomwe anachitilidwa anayamba waiwala, tsono amaona ngat zomwe akumvazo akulota kapena akuonera film yakuNigeria..
Anafika kukampani ya Nkuluyo naona maulemu onse amalandila, anauza antchito ena kuti amusamalire, kunabwera zovala zatsopano namupasa, komanso anamupasa ndalama zambiri kut akagule ndikubwezeretsa zonse anabeledwa.
...
Bambo uyu, anayamika kumwamba kuti ndi zoona chimene uli kufetsa nchomwecho uzatute, Khalidwe labwino suchita zinthu motumilidwa umangothandiza osawelengera kuti azakubwezera chiyani, komanso poti sitidziwa zamawa paja ena anati moyowu uli ngat pelete.
Tiyeni tiphunzire kuthandiza anzathu osowa, ovutika kut Chisomo chathu chichuluke, Bambo uja kandalama komwe amamupasa nkulu wapa wheelchair uja kanali kochepa koma kaamba koti anali ndi mtima opeleka anakolola zambiri, samaziwa kut yemwe akumupasa k20 ndi kwao kwa ndalama...Mulungu akuti tandiyeseni ine muone ngat sinzakusekuliranu mazenera kumwamba.
...
M'bale pamene mtima wako uli okhuzika ndi kuvutika kwaena ndikutengapo gawo kuwathandiza, Mulungu samakusiya kuti uoneledwe zovuta angakhale zitavuta chotani, Mulungu akuti GOLIDE ndi SILVA ndi zanga, kodi nanga amafunilanji tizipeleka, Nkulu wapa wheelchair uja amaziwa kut iye siovutika sakudwala sakupemphetsa, nanga amalandililiranji kandalama kochepako, amafuna ukulu wa Mulungu ounekere monga anenera pa AKOLOSE 4 VS 17, SIKUTI NDITSATA ZOPELEKAZO KOMATU NDISATA CHIPATSO CHAKUCHULUKITSA KUCHIWELUZILO CHANU"
Tiyeni tisatope pakuchita zabwino, tiyeni tikakulitse m'dalitso wathu, tikamusangalatse Ambuye pakuthandiza ena ofunika thandizo kotero kut kwaiye kukalemekezedwe.

  • Share:

You Might Also Like

0 comments