Nyamata wina ankafunitsitsa atagwa muchikondi ndi mkaz wina

By Unknown - February 23, 2018



Nyamata wina ankafunitsitsa atagwa muchikondi ndi mkaz wina okongola kwambiri, koma tsoka ndiilo mkaz anali kukana nkumat si type yake.
...
Nzathuyu amayesesa kuvala bwino, ndalama zomwe amapeza movutikira amayesa kugula tina ndi tina tongosangalasa mkamwa kumutumizira mkaz uja koma ndithu amangonyozedwa ndi mkaz owoneka bwinoyo.
...
Pang'ono ndi pang'ono anayamba kugwa mphwayi osamaikiranso mtima za mkaz uja kufukira mpaka anaiwala.
Basi kenako anafunsila kamkaz kena kooneka konyezeka koma waulemu kwambiri odziwa kupemphera.
...
Ankakhala mwabwino, anayamba kumukonda chifukwa nthawi zambiri amamulimbikitsa moyo wauzimu.
Mkaz okongola uja atamva kut guy ija yagwira Flora msikana opemphera uja, anayamba kuchita nsanje.
Nyamata uja tsiku lina ali khale anangoona message mufon yake.
"HIE EDWARD, NDINE MARIA, KODI WEEKEND IMENEYI MAPLAN AKO NDIOTANI"?
...
Edward sanakhulupirire kuti sms imeneyo yachoka kwa Maria chiphadzuwa mkaz yemwe anali kumukana kumat si type yake.
Sanayankhe text ija, malo mwake anangoimba kuti akhulupire kutidi ndi Maria.
"HIE, ITS YOU MARIA WHO TEXT ME JUST NOW"?
#MARIA : yap, its me, is there any problem?
EDWARD; no no no, ndangodabwa.
#MARIA: ndiye tayankha weekend iyi muli free, tikufuna tikuyendereni.
...
Edward anazunguzika zedi, anaganiza mwachangu ndipo anati;
"Am SORRY MARIA, WEEKEND IYI NDIKUCHOKAPO NDI FLORA.
#MARIA: forget about that one, akupasani chani amenewo.
Nthawi yomweyo Maria anadula fon.
...
Sopano Edward anali mumaplan oti amulepheretse Flora asabwere, azasangalale ndi Maria dona yemwe amamufunitsa kwambiri muumoyo wake, zinathekadi, anamuuza Flora kut akukawaona ankolo ake ku blantyre sakupeza bwino.
Flora anamupepesa Edward ndikumufunira ulendo wabwino.
...
Maria anafikadi mwankokomo, ali walira wali, milomo ili noni noni ngat wangomaliza kumene kudya zankhuli.
Linali tsiku losaiwalika, Edward ananjoyadi, ndipo Maria anachita kumaliza weekend yonseyo mpka kuzanyamuka lolemba mamawa, kuchokatu friday.
Atangopita Maria, Edward anayesa kumuimbira Flora, koma Flora sazayankha fon, anaona ngat mwina alibusy kuyesanso kanthawi kena koma ndithu Flora sanaitole call ya Edward.
...
Flora anali ataidziwiratu yonse chifukwa nthawi yonse yomwe amasangalala ndi Edward Maria anali atachera camera yake yomwe imajambula zonse, atamaliza anaika memory mu fon ndikumutumizira Flora.
A Edward anaona nkhanga mawanga anataya nkhwali mapeto ake analuza zonse.
Nthawi imene satana amakusata kwambiri, imakhala nthawi yoti uli ndi kena kake uli pafupi kuchita bwino, tsono iye amafuna ulephere zimenezo azikuonenabe ukuvutika, ukupemphetsa.
Ache Edward amakanidwa koma from no where kungouzidwa kut ndikhala mlendo wako kuiwala zonse, osaganiziranso kuti njoka ndiyochenjera inanyenga HAVA, mtima osakwanitsidwa achinyamata tikuluza nazo zinthu. Mtima osakhazikika pachoonadi nkuona tikungopitilirabe kumavutika mpaka kumaganiza ngat Mulungu kulibe. Mkaz tili naye chomakafunira HULE ndi chiyani, SATANA AKUTIGWIRITSA NTCHITO MUDZINA LOTI TIKUNJOYA.
Mavuto ena amakhala ovuta kuwapewa koma ukakhala okhulupirura Mulungu, amakutumizira mzimu oyera nkumakutetezera kumavuto onga ngat amenewa, kumakuululira zinsisi zobitsika zimene oipayo angatikole nazo.
Satana uyu Maria, sanamufune Edward momwe anali single, Njoka ija sinanyenge Hava kaamba koti amamva njala, zonse zinali zilibwino koma anabwera ndi nzeru yake ndipo anachimwa, Maria anabwera ndi nzeru yake ngat yachikondi kufukira Edward anachimwa..
M'bale chengera kwambiri ndi awo ukuti ndi anzako, m'dani Okulozetsa mfuti alibwino kusiyana ndi friend okumwetulira koma kumbuyo atabitsa MPENI.
Nthawi zonse achinyamata ngat mwafuna DONA lingalirani mozama MIYAMBO 31 VS 30

  • Share:

You Might Also Like

0 comments