Banja lina litaona zochitika za m'dera lomwe amakhala monga okuba, linaganiza zolemba mulonda.
Tsono nyumba yomwe limakhala banjali, inkafanana kwambiri ndi nyumba ya aneba omwe anayandikana nawo, zonsez zinali ndi dish pamwamba moti nyumba zimenez anthu akangowatchula kuti Kumadish
...
Chifukwa cha Ku fanana kwa nyumbazi, mulondayo amati akabwera usiku amasokonezeka mutu, moti nthawi zambiri amalondela nyumba ya neighbour yomwe inayandikira komwe amachokera,
koma iye samadziwa, mamawa cha m'ma past 4 kukacha amasesa pa bwalo akatelo kumapita kwawo
...
komatu ngakhale mulondayo amadzitenga kuti akugwila ntchito, abwana ake omwe anamulemba, tsiku ndi tsiku amachonga kuti akujomba (sakugwila ntchito) moti mpaka amaganiza zongopeza mulonda wina, izizi zinachitika kwa mwezi onse.
...
Tsiku la malipilo litakwana mulondayo anafika nthawi yabwino kusanade ndicholinga cholandila malipiro ake, sanavutike kwambiri chifukwa anapeza abwana akewo ali pakhonde, koma abale zinali zomvesa chisoni abwana ake atatulusa buku ndikumuonesa
kuti wakhala akujomba kwa mwezi onse.
...
Mulondayo anayesela kuwakumbusa Abwana akewo kuti amkasesa pa bwalo lawo koma abwanawo anakana ndipo yekha anakhulupiranso pakhomo pali biiiiii ndipo anamuuza kuti bwalo lomwe amasesalo ndila neighbor silawo.
Mulonda anabwelera opanda malipilo, m'mene ndikukambamu ndamusiya akupita kwa aneba aja kut akangoyesa kuwauza koma sindikudziwa kut zikathekako chifukwa abwanawo ndikunena anebawo ali ndi khalidwe losalipira antchito what more oti sanamulembe.
...
M'bale ndi Chimodzimodzi moyo uno anthu tikulimbika kugwila ntchito ya Mulungu ndi cholinga choti tikalandile mphoto inde moyo osatha pakutha pa moyo uno (Mateyu 5 vs 12), nayenso satana wapanga ma tchalichi ake ali ndi anthu ake omwe mumaonekedwe
akufanana ndi nyumba za Mulungu akumatchulanso dzina la Yesu koma mphamvu yake anayikana.
Mosadzindikila kanthu anthu tikupemphera mnyumba zimenezi kumayesa nyumba ya Yehova. Moti timakhala tikuimba matamando kumwamba kwa atate oyera, kuganiza kuti tikulemekeza Ambuye koma tikungosesa panyumba ya aneba omwe sanatilembe.
...
Kugwila ntchito molimbika mnyumba zimenezi, koma mwini wake salipira antchito,
zizakhala zomvesa chisoni Yehova akakatikana kuti sitinatumikile iye moyo wathu onse chikhalilecho Ku tchalichi sitimajomba, timapeleka, tikayesela kumukumbusa kuti
takhala tikupemphera ma overnight mu nyumba yake ndipo akatikana kuti nyumbayo siinali yake tikalila ndi kukuta mano. ,
...
Chenjelani pamene mukuchita chisankho maka panyumba zopembezera poti satana sakulola, akuyenda nalo dziko, akubwera ndi maplan ake, otsutsana ndi chiphunzitso choona, Munthu ukalapa moona mtima, Mulungu amatsika nkukupasa chikole cha Mzimu oyera, zikatero sizimadikiranso ena akuuzeni kut ndiinu oyera mtima ai, machitidwe anu okha zimaonetseratu kuti ndiinu owomboledwa.
Mau akuti, Odala Ali oyela mtima chifukwa azamuona Mulungu.
0 comments