Dzina langa ndine Joyce kwathu ndiku Mulanje.. kwazaka zochuluka ndakhala ndikudwala nkhansa yachibelekelo ndipo dotolo anandisimikizila kut sindizabeleka ngakhale ndizalowe mmbanja..
Nditafika usinkhu wabanja ndinapezana ndimwamuna yemwe ananditenga nkumanga nane banja..tinakhala kwazaka zochuluka koma opanda mpahaso yamwana monga adanenela dotolo uja.
Sikulina ndili pa facebook ndidaona uthenga wamau aMulungu ukukamba zachilimbikiso.chifukwa chakukhuzika ndinafuna kuti ndikomente koma mukanthawi komweka fon yanga moto unatha ndipo inathima..
Ndinachita machawi kukatenga fon yamwamuna wanga ndipo ndinaloga akaunt yanga ndikukomenta uthenga uja.. abale kwaMulungu kukhale ulemelelo ndintendele.. patangotha masiku ochepa chikomenteleni post ija ndinanva nkat mwamimba yanga ngat chinthu china chake chikuyendayenda..
Ndinamuuza mwamuna wanga yemwe sanapite patali koma kunditengela kuchipatala. Nditafika kuchipatala mwamwayi ndinapezanaso ndidotolo yemwe anandiuza kut sindizabeleka uja..atandiyeza anandisikimizila kuti ndili ndimimba ya mezi itatu. Ngakhale dotolo anandiuza kut sindizabeleka koma chisomo chaMulungu lelo ndilindimadaliso ochuluka kuposa kuchuluka kwache. Ndinapempha mwana mmodzi koma Mulungu waonjezela pondipasa ana oposela mmodzi.
Abale tiyeni tizikhala achidwi ndi mau aMulungu pakut sakhala pansonga lansingwi kuti tizati azakatikwelele kukatisisila ndiyani?. Mau aMulungu sakhala kusidya lanyanja kuti tizati ndani azatiolokele nkutibwelesela kut tizawakhulupilile?
Khulupilila Mulungu nthawi nzonse.mvela mau ake paliponse pomwe apezeka..
Kwa iwe m,bale amene sunaleme kuwelenga uthengawu, Mulungu achulukise zozizwa zako. Mdaliso wako womwe wakhala ukusekelezedwa kwa zaka zochuluka Mulungu awusegulile muchaka ichi ndikuti uwulandile popanda wokupingapinga.
Mulungu akumane ndi zosawa zako ndipo alowelele pazopinga zomwe ukukumana nazo pakut pawekha sungathe..Ambuye akudaliseni nonse mudzina la Yesu nkhristu AMEN
0 comments