­
­

KODI MUMAPEZA NTHAWI YOWELENGA Baibulo???

By Unknown - February 17, 2018





KODI MUMAPEZA NTHAWI YOWELENGA Baibulo???
...
Nkulu uyu otchedwa William anali ndi ukwati pa 13 February 2014.! Anakonzekera bwino lomwe pa zonse. anagula chilichonse ndipo uthenga unapita Kwa achibale onse kuadziwisa za chikwati chamtengo wapatali. ...
William anali ndi ankolo ake omwe amakhala Ku UK inde tinena Ku united kingdom omwe ndi mponda matiki kapena kuti billionaire omwe atalandila uthenga ot William akupangisa chikwati anali okondwa zedi poti anali mwana yemwe ankamukonda kwambili. ...
Ndipo anamulonjeza kuti azasiya China chili chonse chomwe chingawapangise kukhala busy koma kubwera ndikuzakhala nawo pa ukwatiwo. Komanso anamlonjeza William kuti olo kutakhala kuti anthu onse asabwere paukwatiwo Iwo okha azakwanisa kufupa.
...
Ndipo Iwo anamlonjezanso William kuti azambweresera mphatso yamtengo wapatali. Apa William anadziwilathu kuti ukwati wake uzakhala opambana ndipo anadziwisa okondedwa wake kuti zilibwino pa 14 February valentine day lizakhala tsiku lopambana lomwe Iwo akakhala Ali kuma hotels odula kukasangalala.
...
Tsiku laukwati linafika ndipo anthu onse anali Ku hall ya hotel ina yotchuka Ku Blantyre poti Iwo anasintha hall ya secondary school kupita ku hotel kuti wukwati ukhale opambana.
Kunali anthu ambili koma ankolo a William kunalibe anali asanafike, momwe nthawi inakwana 4 koloko madzulo ankolo a william anali asanafikebe.
...
Apa William anayamba kukaika kuti ankolo ake mwina sabwera zomwe zinamukayikisa kuti ukwati supeza cholowa chomwe chingakwanise kulipira zofunika zomwe anakongola pokhonzekera chikwati. Mwadzidzidzi ankolo a William anafika nalowa mu hall mosakhalisa anafika Ku platform napempha kuti Iwo sakhalisa poti Ndege yomwe anakwera ikubwerera nthawi ya 5 koloko chifukwa cha weather.
...
Ndipo iwo anati ndine wokondwa kubwera paukwati ndipo ndili ndi mphatso yomwe ndikufuna ndipereke. Ndipo Iwo anatulusa bible nati iyi ndi mphatso yamtengo wapatali chifukwa cha nthawi sindinena zambili koma mawa mukatsegule bible ndipo mukawerenge Galatians 5 vs 22 ndimauwa ndingokufunilani banja lopambana. Ndikumanyamuka waku airport.
...
Anthau anangogwila pakamwa poti amayembekezera kuti mphatso yawo ikhala chuma. Kutacha mawa wake William sanalabadireso za bible koma kuyala mnyumba mwawo mphatso zonse anapeza ndipo ananyamuka wautali Ku honey moon patatha four weeks anabwerako ku hony moon ndimmene anaganiza zotsekura bible kuti awerenge chapter chomwe anawauza ankolo awo ndipo atasegula anaona kuti ankolo awo anayika cheque cha ndalama zokwana 20 million mu bible chifukwa Iwo sanafune kuti adzionesere kuti apereka ndalama zambili, apa mpomwe William anathamangila Ku bank koma mwasoka kunali kuti cheque chatha four weeks ndipo chachita expire.
...
William anadandaula kwambili sopano maganizo anali oti akafika kumyumba akawaimbire fon ankolo ake, komatu Ali mnjila analandila fone kuti ankolo ake amwalira pangozi yagalimoto Ku Scotland..
Nyamata anasowa chochita analuza times 2,,,, kodi Muli inu mungatani???
...
Tiye Tiphunzile kusamalira zinthu zopindulitsa pamoyo wathu onse not kusamalira zinthu zongotisangalatsa kwakanthawi kochepa.
Kodi inu katundu amane Mumamulemekeza kwambili Mnyumba mwanu ndi uti?
Nanga mwagula katundu wambili Koma bible muli nalo?
William anathamanga uku ndi uko kut alongosole zacheque koma sizinatheke chifukwa sanazichite munthawi yake.
Mau akuti PATSIKU LOTSILIZA TIZATHAMANGA UKU NDI UKO KUFUNA FUNA MAU AMULUNGU KOMA SITIZAWAPEZA. Chifukwa sizakhala nthawi yake yakumva ndikuchita mau koma nthawi yachiweluzo, nthawi yolongosola cheque inali yomwe ija yaukwati, M'bale nthawi yolongosola moyo wako ndiino osat yachiweluzo, YOSWA 1 VS 8 akut BUKU ILI LACHILAMULO LISACHOKE PAKAMWA PAKO KOMA ULINGILIREMO USANA NDI UTSIKU NDIKUSAMALIRA ZONSE ZALEMBEDWAMO.

  • Share:

You Might Also Like

0 comments