Mnyamata wina anakwera bus yopita m' town.
Atakwera kunabwera munthu wa misala nkuyima pankhomo la bus ija nkumuuza mnyamata anakwera kumene uja "Wamisala iwe tatsika m'menemo"
Anthu anaseka kuti wamisala akumuuza munthu wa bwino bwino kuti atsike m'busimo pamene wamisala ndi iyeyo.
Kenako bus muja munayamba kudzadza anthu ndipo wamisala uja anayimanso pankhomo la bus ija ndikubwereza mau aja "Wamisala iwe ndati utsike m'basimo pompano"
Anthu anagwa ndi mphwete ndizomwe wamisalayo ankamuuza munthu wabwinobwinoyo kuti wamisala.
Kenako Bus inayamba kuyenda ndipo wamisala uja anayithamangira bus ija akukuwa misozi ikutuluka m'maso "wamisalaaa iweeee tatsika m'menemooo!!!!"
Ndipo anthu anankhumudwa komanso munthu uja anakhumudwa kuti wamisalayi mpaka kuchita kuthamangira bus kuti iye atseke.
Kotero mnyamata uja anauza driver kuti ayimitse busiyo kuti iye atsike, ulendowo sapitiliza.
Atatsika bus ija anayang'ana wamisala uja koma sanamuone .
Patapita kanthawi pang'ono kunabwera uthenga woti bus anakwera ija yachita ngozi ndipo onse omwe anali m'busimo amwalira kuphatikizapo ndi driver komanso conductor.
Atamva izi anagwada pansi ndikupemphera kwa Mulungu mosweka ntima misozi ikutuluka m'maso kuti Mulungu wapulumutsa moyo wake potuma ngero wake kudzamutsitsa mu bus.
PEMPHERO.
Mulungu mwini chilengedwe chakumwamba, tikudziwa timakuchimwirani nthawi zonse koma mumatiteteza munjira zosiyana siyana tawonani uyo akuwerengayo ali nayo nthawi yomva mawu anu , mutetezeni ndikumusunga ndi moyo kuti tsiku lina adzalalikire za ufumu wanu, khala nayeni muzonse, yenda nayeni paulendo wake, muusiku mufungatireni ndi manja anu, ngakhale ndiwochimwa koma ndichilengedwe chanu chomwe chimadalira inu nthawi zonse.
Ambiri ali pazovuta zambiri mbiri koma ife lero tikuyamika kuti nthawi ino tili ndi moyo .
Amen
0 comments