­
­

Mzibambo wina amayendetsa track kuchokera lilongwe

By Unknown - February 28, 2018




Mzibambo wina amayendetsa track kuchokera lilongwe amapita mozambigue.
Ulendo uli mkati anawona mzimayi okongola kwambiri. Driver atawona mkazi uja sanachitire mwina koma kuimika Galimoto lija nkukodola mkazi uja.
Adamulankhula pomupempha kuti akwere nawo truck ija mzimayi anakana koma driver anakakamira mpaka mzimayi anakweradi.Driver uja sanachedwe koma kumfunsira mkazi uja mzimayi uja anangoti ndikuyankhabe. Ulendo uli mkati driver anayamba kuona zodabwitsa Mkazi uja anayamba kusintha nkhope ndizovala zomwe.
Driver mantha anamugwira ndipo anapempha monjenjemera kuti mzimayi uja atsike koma anakana ponene kuti wachita kundikakamiza kukwera mu galimoto yako sinditsika.
Mzimayi uja anapitiliza kusintha ndizala zomwe zinayamba kutalika amawoneka ngati Vampaya.
Izi zinamuchititsa driver uja mantha osaneneka zomwe zinachititsa kuti aluze control ya Truck ija ndipo Truck ija inagudubuzikira ku chidzenje chachitali.
MPHUZILO
Abale okondedwa padziko pano pali zokoma zambiri zomwe zitha kutikopa ndikutaya moyo wathu kudzenje lakuya.Komwe ndikuchionongeko.
Kodi inu pomwe mulipo Truck yomwe mwakwerayo ikakuponyani kuti? Kudzenje kodi?
kapena mukafika ulendo wanu?
Chofunika ndikusata mulungu basi kusiya zokoma zapadziko lapansi zomwe ndizamkanthawi kochepa. Mwambuye muli chimwemwe nthawi zonse.

  • Share:

You Might Also Like

0 comments