Zinali zopweteka kwa mayi wina yemwe ankagwila ntchito

By Unknown - February 28, 2018



Zinali zopweteka kwa mayi wina yemwe ankagwila ntchito yokolopa mu ndege kwa dzaka khumi ndi zisanu (15)
koma osapasidwa mwayi ophunzila kuyendesa mwamwayi
tsiku lina ali nkat mogwila ntchito yake anapeza ka buku kolembedwa
"MALAMULO A KAYENDETSEDWE KA NDEGE"
mwachangu anathamangila pampando wa oyendetsa ndegeo
nkuyamba kuwelenga ka buku kaja Atatsegula tsamba loyamba
panalembedwa kuti
"ngati mukufuna kuti ndege ilile tsindikizan batan lofiila"
mayiyu analitsindkizadi batani mpaka ndege inalilima
kenako tsamba lina panalembedwa kuti" ngat mukufuna kuti ndege iyende tsindikizani batani nambala 1
kenako atadina ndege inayamba kupukusa mateyala mayiyu anali ndi chimwemwe poti kunali kuyamba kuendetsa ndege kenako anaona pena polembedwa "ngati mukufuna ndege iuluke mwamba tsindikizani batani loyela mwachangu mayiyu anadina ndipo zitsulo zinayandamadi mlengalenga apa nkuti mayiyu analimo yekha kenako atawelenga tsamba lomaliza panalembedwa kuti "ngati mukufufuna kuti ndege itele kawelengeni buku 2" zinali zachison kuti mundegemu munalibe buku 2 lokamba za katelenge ka ndege (kodi zinamuthela bwanji mayiyu?)

MPHUZILO
Tsono tamvetselan umu ndi momwe zimakhalila pamoyo wathu pomwe satana amatinyengelela pochita tchimo nkumamva kukoma koma zikativuta amatithawa monga zinamchitikila mayiyu koma lelo ndi tsiku labwino m'bale lot upange chisankho ukadali ndi moyo yesu khristu wakonzeka kukukhululukila.
Amen

  • Share:

You Might Also Like

0 comments