YEHOVA ALIPOMPANO..... ABALE TAWELENGANI UTHENGA WOPASA CHIDWIWU.. ............YAKOBO..

By Unknown - February 23, 2018




YEHOVA ALIPOMPANO.....
ABALE TAWELENGANI UTHENGA WOPASA CHIDWIWU..
............YAKOBO..
Ndipo yakobo anafika kudela lina natola mwala nasamila nkugona tulo.. koma pamene anali kugona, analota angelo akusika ndimakwelelo ena akukwela. Ndipo Yehova ananena naye nati.. ine ndine Yehova wa abraham ndi isaki .Ndipo ndizakhala pamozi ndiiwe.chomwecho ndizakubwezela iwe kudziko ili lomwe uzakhalemo iwe pamozi ndi mbewu zako..
Ndipo kunali pamene anauka kutulo Yakobo ananena muntima mwache;; Yehova ali momuno ndipo sindinaziwe. Pamenepo anaopa nanena..poopsa pompano!. Pompano ndipo panyumba yache ya Mulungu. Sipena ai pompano ndipo pachipata chakumwamba..
Okondedwa vumbuluso ili ndilofunika kulinvesesa bwino. tilipo ambili lelo timati ine sindingapemphele chifukwa ndili ku jon ndizakapemphela ndikazapita kumuzi chifukwa ndikomwe kuli tchalitchi changa..
Mau awa amangokhala ozinyenga tokha maka posalingalila zatsiku lakufa kwathu..nkutheka imfa yako ikupeza udakali ku jon komweko usanabwele kumuzi kuzalowa mtchalitchi chako. Nanga ukafa usanalape akakuyankhile ndindani mlandu wako?
Ena tikachimwa timati tizalapa siku lathu lopemphela tikazapita ku tchalitchi..koma nanga imfa itakutenga siku lakutchalitchi lisanakwane ndindani azaime nawe kudzanja lako?
M,bale wanga pamene ulipo ndipo panyumba ya Yehova. pomwepo ndipo pachipata chakumwamba .kaya ukudusa munkhalango yoopsa, kaya Njila yaminga yoboola nsapato , kaya nyumba yako ndiyopanda chipinda. gwada nupemphele ndikulapa machimo ako. monga anaona yakobo nati, pompano poopsa pano, Yehova alipompano ndipo pano ndipo pachipata chakumwamba
Mau awa anaphelezela kutiziwisa zatsiku losiliza lomwe ena lizatipeza tili kumunda .ndipo ngat lizatipeze titalapa kumunda komweko thambo lizasekuka ndimakwelelo azatisisila. Malemba oyela amasikimiza zasiku lachimalizilo kut..iye wakusambila kunyanja azakhala ali chisambile, iye wakufolela nyumba azakhala alichikhalile padenga soka kwa iye amene tsikuli lizamufikile asanalepe chifukwa sazachiona chipata chakumwamba..
Kunva uthenga pa fb nkuunyozela wina nkuwutenga nkuzimangila nawo nyumba yake Yehova nkuzafikilamo nkukapulumuka. pamene iwe unaukana nkumati pa fb palibe tchalitchi. Tisamale kuopa kuzagwila chikolopa
Odala iye amva mau aMulungu nawasunga ndikuwachita pakuti azimangila yekha nyumba yokhalamo Ambuye .koma soka kwaiye wakunyalanyaza pakut ayanjana nayo gahena yamoto..

  • Share:

You Might Also Like

0 comments