Bambo wina anali ovutika, akati wadya ndiye kut wapemphesa pena wagwira ganyu ndipo malipiro ake kupasidwa chakudya basi.
By Unknown - March 28, 2018
...
Nkulu wina anali kukhuzidwa kwambiri ndi moyo wa bamboyu..mpaka anamufunira kwina kwake kwabwino ndipo anakalembedwa ntchito...
Anthu ena atamva maganizo ankuluyu anayesa kumulesa, kumupekera nkhani kut asamuthandize bamboyi cholinga azikawagwirilabe maganyu awo namamupasa tichakudya, koma nkuluyu sanamvere.
...
Koma angakhale Bamboyu amagwira ntchito kumeneko nkumalandila, amavutikabe, amapitabe kumakagwira maganyu aja ndipo sopano mavuto anaonjezereka chifukwa zinali ngat alindi malo awiri ogwira. Amapezeka otopa thupi lake silimaonekanso bwino.
...
Tsiku lina nkulu anamuthandiza kupeza ntchito uja, anamuyendera namupeza kut akuvutikabe, mavuto sanathe ndipo anamufunsa;
"KODI SIMULANDILA NDALAMA KUTCHITO KUJA"?
Bamboyo poyankha anati;
"Miyez yonseyi ndakhala ndikulandila, ndipo ndalama zake zilipo zili nyumbamu"..
...
Nkuluyu anamuuza kut;,
"NTCHITO YANDALAMA SIKUSUNGA KOMA KUGWIRITSA NTCHITO"
Anamuuza ntchito zambiri zandalama ndipo bamboyu anakondwa kwambiri ndipo anayamba kuoneka munthu otsinthika.
...
Funso nkumati, kodi kucharichi ku mzikiti timapita every week, m'dalitso, Yesu yemwe timalandilra timamugwiritsa ntchito??,poti tikuoneka kut tili nsinga za satanabe, Yesu ndi thandizo lathu lopezekeratu panthawi yamavuto,ambiri tili naye mtimamo koma tangomutsunga ngat bambo uja, IYE AKUT MUNDIITANE INE NDIPO NDIZAKUYANKHANI NDIKUKUONETSANI ZAZIKULU ZOMWE SIMUDZIDZIWA
Tatiyeni lero abale timugwiritse ntchito Yesu wathu pavuto lililonse ndipo ali okhulupilika kutithandiza akungodikira pemphero lathu kuti achitepo kanthu, ndi chikhulupiro mu mwaz waYesu chilichonse nchotheka.
Anzathu ena pa MARIKO 4 vs 35 anamuleka nkugona pang'onong'ono akanataya miyoyo yao.pamtendere, pamavuto tiyeni timuyankhule Yesu wathu.
0 comments