Nzungu wina ankayenda munkhalango ndi mwana wake wanyamata wokulilako ndithu..
Akuyenda choncho anaona nkango ukubwera kutsogolo kwao.
...
Mwana uja anawakumbatila bambo ake, anali ndi mantha akulu ndipo ankaganiza kuti kwao kwatha basi, afa.
Koma anadabwa kuona bambo ake aja sakudandaula, akuyendabe kumayandikira kukumana ndi mkango, m'menemo nkut iye atawakhumbatila kwambiri asakuona zomwe zikuchitika.
...
Kenako anafuna kut aone zomwe zikuchitika ndipo anaona bambo ake akupanga tima sign kuonetsa mkango uja, anapinda zala zitatu nkusala chachikuli ndichosiliza chakumapeto, ndiye amauonetsa mkango uja kwinaku akukhala ngat akutembenuza zanja , kufikira mpaka mkango okha unagona pansi iwo nkudutsa nkumapitilira.
...
Mwanayu anachita chidwi kwambiri nzomwe anachita bambo ake, koma sanafunse kapena kunena chilichonse.
Atafika malo ena, bambo ake aja anamusiya mwana uja malo ena kut azipumulira, Iwo nkupita gao lina kumakajambula zina ndi zina...
Mwana uja ali khalee kwinaku akudya anaona Kambuku akubwera straight pomwe anali..
...
Mwana anasowa chochita, koma mwachangu anakumbukira sign yomwe bambo ake anachita kwa mkango uja, nayenso anayamba kuchita sign ija, koma Kambuku sizimamukhuza, anayesa kupanga ndi mtima wake onse kutembeniza zanjali koma ndimomwe Kambuku amaimika ubweya wapakhosi kusonyeza ukali...
Mwa mwai Bambo ake aja anatulukira ndipo ataona izi anathamanga nkumuika mwana uja kumbuyo kwao, ndipo anayamba kupeleka sign ina yosiyana ndiyomwe anachitira ndi mkango, apapa amakhala ngat akufuna kuloza kambuku uja pamutu koma amayendetsa yendetsa nkonou, kufikira Kambuku uja ukali unachepa ndipo anamulozera tchire lina Kambuku ananyamuka nkumapita.
...
Mwana uja anangot kakasi kumangowayang'ana bambo ake kusowa chonena.
Sign yomwe inapelekedwa kwa mkango inali yosiyana ndi sign yomwe inapelekedwala kwa kambuku.
Ambuye Yesu atatulusa ziwanda zoopsa anapeleka SIGN ndipo ziwandazo zinakalowa mu NKHUMBA...mwina zikanakhala kut zinali pafupi ndi NG'OMBE sign yomwe akanapeleka ikanakhala yosiyana ndiyomwe anachitila ndi nkhumba..
M'neneri ELIYA analandila Namani wakhate mfumu yaikulu yochoka ku tsidya la Yolodano, koma sign yomwe anapeleka Mneneriyu ndiyakut akasambe munsinje kasanu...
Sionse amene amauzidwa kut akasambe munsinje, koma sign ya NAMANI kuti atchire ku KHATE lake linali loti akasambe munsinje.
...
Lero lino abale tili ndi sign yomwe tiyenera kutchita ngat taphinjidwa ndiye kuyang'ana kumwamba mwachikhulupiriro.
Ndiye ukayang'ana kumwamba mwachikhulupiro Mulungu amakutumizira mzimu oyera nkukulondorera kwa aneneri kuti ukalandile chosowa chako....
Tsono vuto lagwa lero ndiloti, anthu sitikukhazikika pachimodz, Pamene aneba athu alandila m'dalitso wao kuzera mwa aneneri akumpingo kwao, ifenso tikufuna tipite komweko ati tikalandile chosowa chathu...
Kutero anthu lero ali pewu pewu sakuziwa chomwe akuchita, ati kaamba anamva kut mpingo umenewo wina wake anapeza banja naonso akufuna akapeze banja kumeneko, sign yogonekera matchimo anu, singafanane ndi sign yochosera umbava wanga chemwali, nkhani sikusintha mipingo koma ndikudikira mwachikhulupiro ndipo yekha Mulungu azakusonyesa SIGN yako ndipo uzabooleza...kupemphera kwama prophet ochuka zilibe kanthu, nkutheka sign yoti mumasulidwe silikumeneko ndipo muzingotaya nthawi...
Ndinanenapo kut Munthu ukalapa tchimo, sizimangochitika nthawi yomweyo mpka kuyamba kuona zokoma za Mulungu, zilingat kulembedwa ntchito, sumalandila malipiro tsiku lomwelo, ndiye lero anthu tikalapa malo modikira mwachikhulupiro pamene Mulungu akufuna kuyendera moyo wathu timaona kuchedwa, mpaka kuthamangila kumpingo wina chifukwa wina wakuuzani kut zamuyendera, koma simukuziwa kut iyeyo wadikira kwanthawi yaitali bwanji? SIGN yogonekera mkango ndi SIGN yogonekera kambuku inali yosiyana..koma munthu opeleka ma SIGN yo Anali m'modz...
M'dalitso wanu sungabwere nthawi yofanana ndi m'dalitso wanga koma opeleka m'dalitsoyo ndi m'modz yemweyo MULUNGU... Iye alindinyengo zake zimangotengera nthawi ikakwana, osathamangila..
.pakut ziliko zambiri zooneka zaumzimu koma zikusogoleledwa ndi oipayo...Mwana uja anapeleka SIGN kwa kambuku koma sizinatheke...mukhoza kupempheredwa koma ngat SIGN yamachilitso anu sili kumeneko...muzasintha mipingo mpaka kale.
0 comments