KWA M'BALE IWE UKUKHALA KUDZIKO LAKUTALI CHENJERA. ...

By Unknown - March 03, 2018





M'mamawa wa Lolemba la tsiku lina, uzaona ngat ukulota.
Uzaona mkaz wako wako ataika zinthunzi zokongola kwambiri ali mu wedding dress kwinaku atanyamula Maluwa m'manja mwake.
Kudzanja lake la m'manja kutaima nyamata wantali pang'ono ataponyeza suit yapamwamba atamugwira mkaz wakoyo mchiuno kwinaku akumwetulira ngat kunja kuno kulibe mavuto.
...
Uzayesa kuchichita zoom chithunzi chimodz koma suzakwanitsa, thupi lako lizachita thukuta, uzasiya cup ya tea pansi ndikukankhila uko mbale yamadzila osaphatikiza ndi bread.
Uzasowa chochita koma kenako uzaganiza zoti umuimbile fon koma uzapeza kuti sikupezeka.
Uzaganiza zomuimbila mlamu wako yemwe ndi mlongo wake wa mkaziyo, koma azakuuza kut umuimbilenso chifukwa akuyendesa galimoto akukasiya aband.
...
Mtima wako uzadumpha kwambiri, uzafuna kut umve kut abandiwo amaimba kuti koma zachison maunits ako azathera panjira.
Uzathamangila kushop ndicholinga choti ukagule ma units umvetsetse chomwe chikuchitika kumudz koma uzapeza kuti shop yo sanatsegule. Mutu wako uzazungulira kwambiri, nthawi yomweyo uzakumbulira kut mu wallet yako ngat dzulo lake unasungamo ma units, ndipo uzaganiza zochita mwachangu kuti ukatenge ma units kunyumba kwako kenako uthamangile kuntchito.
...
Bwana ako azakuimbira uli paulendo opita kunyumba kwako, koma uzamuuza kuti wasala ndi 2mins yokha kut ufike, uzayamba kuyenda chothamanga koma kufika kunyumba kwako uzapeza kuti nkokiya SUTHU yemwe Umakhala nae wachoka poti amaganiza kuti wapita kuntchito watenga ma key ako.
Suzalola kuti unyamuke uzipita kuntchito osatenga maunits aja komanso ka lunch box, uzamuimbira SUTHU fon koma azakuuza kuti ali ku clinic ndipo atumiza munthu ndi ma key, uzadikira koma munthu yo sazafika nsanga, uzaona nthawi, uzapeza kut yatha, uzaganiza kuti bwana wakwiya nawe basi uzaganiza zongojomba.
...
Munthu wama key uja azatulukira uzaoneka mokwiya kwambiri, uzawatenga nkutsegula nyumba nkutenga ma units nkuika mufon, Nthawi yomweyo uzaganiza zoimbira sister wako, azakuuza kut umuimbilenso pakatha 3hrs chifukwa ali ku immigration akuwapangisila ana ako awiri ma passport kut azibwera komwe uli, pakuti posatila ndi chikhalidwe chanu mai a ana wo omwe anali mkaz wako sangawatenge pakuti akwatiwa.
...
Uzafuna kut umve bwino bwino, koma azaidula. Uzapuma ngat mbawala yotopa pothamangisidwa, uzaganiza kuti umuimbire brother wako koma azakuuza kuti ali ku LILONGWE Sakudziwa chilichonse, uzafunsa za fon yamai wako kut nchifukwa chiyani sikugwila, azakuuza kuti fon yao inafa 2016 mu june, uzazimvera chison kwambiri ndipo uzadula fon, uzakhala pheeee kuganiza kut mpaka watha 2yrs osadziwa kuti fon ya mai wako inafa, osawambila.
Uli nkati moganiza momo uzamva kugogoda pachitseko, uzapeza kuti ndi mkaz wachisuthu uja ali wachimwemwe kwambiri.
...
Azabwera pafupi nkukupanga "CONGRATUATIONS" Uzadabwa kwambiri, azabwera pafupi nkuunong'oneza mwachikondi kukuuza kuti " AM PREGNANT" Uzanyatsidwa kwambiri ndipo uzamukanka mpaka kugwera kuchitseko, uzamuuze kut sukuziziwa za mimbazo, azachoka akulira iwe poganiza uzaona ngat wapita kwa nkulu wake yemwe amakhala kungodumpha nseu.
...
Uzatenga fon yako nkuyamba kuona mafoto ankaz wako omwe amaoneka kut dzulo dzulo lakelo wakwatitsa oyera...mosakhalitsa uzalandila fon yochokera kwa bwana wako, azakufunsa chifukwa chomwe sunapitile kuntchito, koma uzasowa choyankha, azakuuza kut shop yakhala yosasegula pakuti iye amachokapo ndipo utamuuza kut wasala 2mins anasiya ma key ku shop yoyandikana nayo kuti ukafika utsegule.
Uzalira kwambiri poganiza kut limenelo likanakhala tsiku lako loweluka chifukwa ukanaba ndalama nkuthawa, bwana yo azakuuza kuti sakukufunanso amadana ndi anthu achibwana.
...
Uzaona ngat dziko lakuda, uzasowa ntengo ogwira, uzagona pabed chagadaaa misoz izayamba kutuluka yokha, koma kanthawi komweko uzaona kut nyumbamo mwalowa anthu, ukazadzuka uzapeza kuti ndi apolice mosogozedwa ndi Suthu uja wakakusumira kuti umamumenyea NKHANZA KWA AMAI.
Azafuna aone passport yako koma uzawauza kut inataika, azakutenga ulendo waku station ndipo azakusekera mu cell asanakutenge startment, uzakhalamo 4days ndipo neba wako yemwe umagwirizana naye kwambiri azabwera kuzakuona ku policeko, azakuuza kuti mkaz wako (SUTHU) uja akukhala ndi wapolice yemwe anabwera naye kunyumba kwako kuzakumanga, uzadandaula kwambiri kumva kuti akumavala zovala zako, uzayang'ana mucell monse, kufunafuna chingwe choti uzikhweze nacho koma suzachipeza, mpomwe uzaziwe kuti NO BODY CAN STOP REGGAE.
...
Tiyeni abale tikakhala moyenda, tizikumbukira kumudz, tiyeni tiwakumbukire anzathu omwe tinavutika nao limodz kupeza ndalama ya passport komanso transport, zilibe kanthu kuti mumagwira nokha ntchito koma mumavutila nonse kudya matemba cholinga ndalama ikwane, bambo ayende ulendo khomo litsinthe kukhale ngat momwe kulili kwa aneba.
Koposa osaiwala Mulungu kaamba mulikuchilendo pakuti anati MUSASIYE KUSONKHAKA PAMODZ, sanachule kut mukhala kwanu kokha ai koma paliponse ndi kuli konse.

  • Share:

You Might Also Like

1 comments

  1. Hi. Sir.. You really are a genius, I feel blessed to be a regular reader of such a blog Thanks so much.. -Online kaj💕💋 font copy and paste what is love?

    ReplyDelete