Kwao kwa Rabecca kunali agalu akulu akulu owopsa

By Unknown - March 25, 2018



Kwao kwa Rabecca kunali agalu akulu akulu owopsa, koma chodabwitsa Rabecca Samafika kwao kwa Monica ati kaamba kunali agalu...
...
Anzake ankamuseka kwambiri chifukwa choti agalu akwao anali owopsa kusiyana ndi agalu akwao kwa Monica...
Anzake akamufunsa kut;
KODI IWE UKUOPA AGALU MESA KWANUNSO KULI AGALU"???
Nthawi zonse samayankha zomveka, pena zimakhala ngat kuti watutumuka ndifunsolo, tinene kuti amaziiwala kuti kwaonso kuli agalu.
...
Malo mwake iye amati;
"AGALU AKWATHU, SIOTI UNGAWAIKE MUGULU LA AGALU, NDIMATHA KUWAKWAPULA, NTHAWI ZINA OR KUWAKWERA NGAT BULU."
Komatu anzakewo anamuuza kut chimenecho nchibwana,,galu ndi galu tsiku lina azasimba tsoka atamuluma..
Koma Rabecca anangotseka, sanasiyebe zomwe amachita ndi agaluzo...
...
Ndiye kaya tsiku ili agaluwo anali asanadye, Rabecca anati ayambenso zake zachibwanazo koma akanaziwa,,galu anamudumphira nkumukanda kumaso kuchoseratu chikopa...momwe ndikunena pano Rabecca wagonekedwa muchipatala akulandila thandizo lamakhwala,,agalu amuvulaza si akwa Monica omwe amawaopa ai koma omweo akwao omwe iye amati sali mugulu la agalu.
...
Anthu ambiri tili ndi mkhalidwe losinjirira matchimo omwe amachita anthu ena, kuiwala kut ifenso siife oyera.
Tikafika pa facebook kupeza anthu akukamba zamavuto awanthu ena uhule wamunthu wina, kuba kwa wina zimakhala ngat iwowo ndi angelo.
Komatu baibulo limati
"TIKATI TILIBE UTCHIMO, TIZINYENGA TOKHA NDIPO MWAIFE MULIBE CHOONADI.
Anthu tilindi agalu olusa koma tilibusy kukamba za agalu akwa neba, Tchimo lozolowera limaoneka lophweka limaoneka lopepuka ngat momwe amamvera Rabecca za agalu omwe anali akwao mapeto ake anamuvulaza..M'bale anthu omwe umawasinjirira kut ndiochimwawo akhoza kuzalapa koma kuzakudabwa iwe oyerawe ukupita kugahena...
Yesu anati Ochimwa akhoza kuzalowa muufumu waMulungu koposa omwe timaziona ngat akhristu lero lino, tili ndi agalu athu koma sitikuwaopa tikuona ngat sangatiphe achepa, kutero fodya yemweyo, uhule omwe omwe mukuona ngat simukuonedwawo, kuba komweko mukut mukuba zam'boma zakampanizo nzomwe mukaocheredwe,,nyanga zomwezo mukut zimakutetezanizo nzomwe mukapsere chifukwa mwakhulupira zimenezo kuleka kukhulupira Mulungu...
Tiyeni tisanayambe kuopa agalu akwao kwa Monica tiyambe taopa agalu athu,;pakut ndiomwe azatipweteke kukatilowetsa kuchionongeko..

  • Share:

You Might Also Like

0 comments