...
Chi khristu kapena chipulumutso osachitenga mwachizolowez, Kuti moyo wako ukhale ukulamulidwa ndi Mulungu, Kuti dzina lako lilembedwe mubukhu la Moyo sichinthu chamasewera.
...
Pamene munthu waganiza kusiya ZOIPA, kusiya UHULE KUBA ZAUFITI ndi zina zotero, ndikulandila Yesu kukhala Mbuye ndi mpulumutsi wamoyo wako, dzina lako silimalembedwa nthawi yomwe mubukhu la Moyo, dziwani kuti MULUNGU sanamizika.
...
Pamene walapa Mulungu amakhala akukuonetsetsa machitidwe ako, nthawi iyi ndi nthawi yovuta chifukwa umakhala ngat uli pakati pakati, ndinthawi yomwe umavutika nao mayesero, akaz omwe amakukana amabwera okha nkuzakupasa program, nkukuuza kuti osadandaula za ndalama zonse akapeleka....ndinthawi imene amuna odula ma Cerebrity omwe umakhumba uatagonana nao koma amakusasa kuti iwe si type yao, umaona akukuimbira fon cholinga chimakhala kukuletsa kumoyo osatha komwe ukupita.
...
Tsono ukalimba mtima nkuthana nazo zonsez mothandizidwa ndi mphamvu yakumwamba, mpomwe Mulungu amatsika kumwamba ndipo amazakupasa chikole cha NZIMU OYERA ( welengani machitidwe 1 vs 8) ndipo kuchoka pamenepo umakhala bwenz la Mulungu amakugwiritsa ntchito umakhala wa ntendere ndipo umayamba kuona zabwino zabwino zikubwera pamoyo wako. (Welengani YOBU 22 VS 21)
...
Tatiyeni tionenso nkhani ya YUDAS SCARIOT NDI CHIIGAWENGA CHA PA MTANDA. .
Mukuziwa Yudas scariot amayenda, kucheza komanso kudya limodzi ndi Ambuye Yesu Khristu mwana wa Mulungu wa kumwamba koma Yudas mwai umenewu anawupeputsa, anautenga mwachizolowez.
Yudas amayenda ndi Yesu koma mkati mwake munalibe Yesu.
...
Sizachilendo kuona izi kwa Yudasi, Ambiri lero lino tikukangalika kupita ku church komanso kugwira ntchito za uzimu koma sitili ma bornagain enieni, Sitikumuzuwa YESU. ngakhale tikumagwira ntchito za mpingo ngati kulalika, kupereka chakhumi, kuvina kapena kulambira mu church koma tikadali osapulumutsidwa. Yudas amagwira ntchito za uzimu ndi Ambuye Yesu amachilitsanso koma sanali bornagain weniweni. Yudas anali okuba(Yohane12:6).
...
Yudas amatumikira Yesu koma amachitabe uchimo. Chi khristu chimenechi ndi chomwe chili pakati pa akhristu mu nyengo ino koma nditsindike kuti ndi chi khristu choopsa. Ndi ngozi chifukwa chibalo chake chizakhala chowawa pa tsiku lomaliza.
...
ZACHIGAWENGA
Tamveserani tsopano za chigawenga cha pa mtanda: dziko linamuweruza kuti ndi munthu oipa oyenera chilango cha pa mtanda koma mphindi yomaliza yomwe anamuziwa Yesu ngakhale anali kale pakati pa chiweruzo cha dziko, anagwiritsa ntchito mphindi imeneyo pano ali ndi moyo osatha. Wina kumakhala, kumayenda mpaka kumadya ndi Yesu yemweyo koma kumachipeputsa chinthu chimenecho. Pa Mateyu 21:31 Yesu akuyankhula mu kachisi kuti anthu omwe amaoneka ngati ndi ochimwa kwambiri ngati ma hule ndi amisonkho azakalowa kumwamba, akhristu okangalika ndi utumiki kumabwera pambuyo pawo. Why? Tili busy kugwira ntchito za Mulungu koma tikadalinso mu uchimo! KUCHITENGA CHIKHRISTU MWA CHIZOLOWEZI.
...
Kumapemphera koma kumakhalabe moyo wa uchimo! Chi khristu chimenechichi ndi choipa. Kupanda kusintha mkwatulo kubwera, anthu azatsala ochuluka koma ali anthu olimbikira za uzimu, wina yemwe amaoneka ngat sapemphera chisomo chizamugwera mphindi yotsiriza kumva mawu mkusiya uchimo posakhalitsa ndikukwatulidwa kukalowa kumwamba. Dont take salvation for granted. Be very careful every minute. Utha kulembedwa mu buku lamoyo mamawa koma pofika masana mkuchotsedwa ngati uchidoda chi khristu ngati mmene anachidodera Yudas. ...
Kumakhala mu mpingo koma kumachitabe za uchimo ndi chibwana. Nthawi yomwe ukuseweretsayo wina yemwe anamwalira asanalape amayilira. Amafuna atapasidwa even just a second kuti alape koma its too late. Lapa zenizeni before its too late. Sungakhale kapolo wa mabwana awiri. Modzi akhumudwa. Usasakanize chi khrsitu ndi uchimo.
Pa chivumbulutso chapter 3 Yesu ananenetsa kuti anthu opemphera koma kumachtanso uchimo azawakana. Anati azawalavula.
Chita chifuniro cha Mulungu (mateyu7:31). Yesu ndi oyera sungamusakanize ndi ti ma trouser tothina, chamba, kukhwefula, kumeta zosalongosoka, kuba, kunama, miseche, zibwezi zachabechabe, magemu, kulambira choumba mkumati Yesu, ma legens pa mtunda, chigololo, matama, mowa, kulephera kupita kopemphera chifukwa cha mpira.
...
Munthawi ya NOWA nso zinkaoneka ngat zocheza zongosautsa moyo momwe ankasema chombo kwinaku akulalika zanthawi yoopsa yomwe ilikubwera, koma anthu anasankha zikondwerero kukwatilana kulezera kuphana monga momwe zilili lero, M'bale imva mumtima mo kut Gahena ilipodi ngat sunalape, gwada pansi ndikulandila Yesu kuti uziyenda moyo wako uli opulumutsidwa.
0 comments