LUCIUS BANDA.

By Unknown - March 31, 2018




LUCIUS BANDA.
.
Sizabwino kulemekeza munthu akamwalira, tiyeni pamene alimoyo tiziwathokoza pa ntchito zina zotamandika zomwe anagwira.
Lero tiyeni tiwone mbiri ya Lucius Banda yemwe mozinyadila amazitchula kuti ndi Soldier.
.
Lucius Banda anabadwa pa 17 August chaka cha 1970 mudzi mwa Sosola, Group Village headman Kapalamula, mfumu yaikulu Nsamala ku Balaka.
Anaphunzira maphunziro ake a ku Primary pa sukulu ya Mponda yomwe ili pafupi ndi Parish ya Balaka.
Lucius Banda Maphunziro ake sadathele ku Primary, anapitiliza mpaka ku Secondary school.
.
MOYO WAKE MU MUSIC
.................................................
LUCIUS Banda anayamba kuyimba chaka cha 1983 menemo kuti ali ndi zaka 13 ndipo adali ali ku primary school.
Ndipo yemwe anali kumuthandizila pa mayimbidwe ake anali chimwene wake Paul Banda yemwe ndi tsogoleri komanso yemwe anayambisa gulu la Alleluya Band.
Lucius Banda anayimba pa stage koyamba pamaso pagulu mu chaka cha 1985 ndipo panthawiyo anali nawo mugulu la Alleluya Band mosogozedwa ndi Paul Banda.
.
Malingaliro ofuna kutukula luso lake anamuzela ndipo anaganizila zopita ku South Africa kuti akaphunzile mayimbidwe ndikupitisa patsogolo luso lake.
Maloto ake anakwanilisidwa pomwe mu chaka cha 1993 anajowina gulu lina la ku Johannesburg Lotchedwa DORKEY HOUSE ndipo kumeneku anakhalako chaka chimodzi.
Anajambula Album yake yoyamba yotchedwa "SON OF A POOR MAN" ndipo anajambulira ku Standel Music Studio, producer wake anali George Arigone wa ku Argetina. Ndipo omwe anamuthandizila ma backing vocals anali Nomahalanla Nkhize komanso oyimba wina wa nyimbo za uzimu Debora Freser.
Album imeneyi munali nyimbo ngati ''MABALA, GET UP STAND UP, LINDA, AND LIFE ON EARTH''.
Nyimbo ya Mabala inatchuka kwambiri. Nyimboyi inali yandale yomwe imafotokoza za nkhaza zomwe zinalipo mu ulamuliro wa Malawi Congress Party. Nyimboyi inali ndi mawu oti;
''kukhululuka ndiye takhululuka, koma mabala ndiye akupweteka.....
Kenako amazati;
''tavesela iwe zanga olira, nkhuku ija yafa, mdima wathawa ndipo nyali yawala..''
Ndipo chorus yake amazati;
''inu mumati zizakhala chochi, mpaka liti abale? Ana a Mulungu sangakhalire kulira masiku onse a moyo wao''...
Kuyivesela bwino nyimboyi, inali yolira komanso linali pemphero.
.
1994, Malawi Congress Party inachoka m'boma ndipo ufulu wa mayimbidwe unapelekedwa.
Mongokukumbusani, Nthawi ya Malawi Congress Party samalora munthu kuyimba nyimbo mwachiswawa. Munthu ukajambula nyimbo yako, imayenela iveseledwe kaye ndi akulu akulu a boma ndipo kenako akupase chilolezo kapena nyimbo yakoyo amayikana kuti siyololedwa kuyimbidwa muno Malawi.
Nthawi inayake oyimba winawake wa ku America anayimba nyimbo yotchedwa ''Ceicilia please come back, I'm down on my knees''
nyimbo imeneyi inangolira kamodzi pa MBC koma yemwe anayisewela pa Radio pa nthawiyo ntchito inawuma ndipo nyimboyi inalesedwa kuti isazavekeso chifukwa munyimboyi munali dzina la Mama wa fuko la Malawi.
Koma 1994, ufulu unapelekedwa ndipo oyimba anayamba kuyimba nyimbo mwa ufulu.
.
1997, Lucius Banda anatulusa album yake ya nambala 4 ndipo imeneyi mutu wake unali ''Yahwe''.
Mu album imeneyi munali nyimbo monga; ''Njoka mu Udzu'' nyimbo yomwe imadzuzula mabwana ma office. Munaliso nyimbo monga; ''MUKAWAUZE" yomwe imakumbusa anthu za nkhaza za Malawi Congress Party. Nyimbo ya ''Mukawauze'' chorus yake imaveka chochi;
....mukawauze anawo asatengeke, njoka ndi njoka singasinthe manga.........
Ndipo album yomweyi ya Yahwe munaliso nyimbo yomwe anayimbila malemu mayi ake yomwe imati; ''chabwino mayi zembani, mupume mu mtendere, kumwamba muli amayi mukoze malo anga....
Ndipo kenako chaka chomwechi Lucius Banda anakhazikisa gulu lake loyimba lotchedwa Zembani Band.
.
Gulu la Lucius la Zembani Banda linatulusa oyimba ambiri omwe nthawi inayake anatchuka kwambiri monga; Billy Kaunda, Enort Mbandambanda, Mlaka Maliro, Charles Nsaku, Pat Abig Tung'ande, Emma Masauko, Wendy Harawa ndi ena ambiri kuphatikizapo Lameck Katunga komanso Dan-Lu.
.
Lucius Banda ndi oyimba oyamba wa kuno ku Malawi kuyimba nyimbo zozuzula Ngwazi Kamuzu Banda mu nthawi ya ulamuliro wa chipani chimodzi.
.
MOYO WANDALE
.....................................
Lucius Banda ndi phungu wa kunyumba ya Malamulo wa chipani cha UDF.
Kanthawi kenakake, Lucius Banda analamulidwa ndi court kuti sali ololedwa kukhala phungu wa kunyumba ya malamulo chifukwa choti analibe mapepala a form 4.
Lucius Banda mu 2005 pomwe malemu Bingu ndi Muluzi ubale wao sunali bwino, iye anayimba nyimbo yoti ''njobvu zikamamenyana umavutika ndi udzu chonde tagwilizanani''
inali nyimbo yabwino kwambiri chifukwa munali uthenga wa mtendere zomwe zinasonyeza kuti mkuluyu ndi wa mtendere.
.
Nthawi inayake anadana ndi Bingu ndipo anayamba kuyimba nyimbo zonyoza Bingu, mpakana anamangidwa. Koma atamwalira Bingu, Lucius analiuza dziko kuzela mu nyimbo yake kuti Bingu anali mamuna olikonda dziko.
.
Lucius Banda adakayimbabe ndipo ndi Legend wathu pa mayimbidwe.



  • Share:

You Might Also Like

1 comments