Ngati kuli anthu ena omwe anaona ukulu wa MULUNGU, analandilandila m'dalitso omwe samayembekezera m'modz mwaiwo ndi David,
By Unknown - March 31, 2018
Davide anali Munthu onyozeka pantundu wakwao, nthawi zonse kwake kunali kutchire kodyetsa ziweto.
...
Angakhale pazokambilana Davide samaloledwa kupeleka maganizo, amati;
"INUNSO MUNGATIUZE CHIYANI"
Komatu chomwe amachita Davide samakhumudwa malo mwake amakhala akulemekeza Mulungu kufikira Mulungu anati;
"NDAMPEZA DAVIDE MTUMIKI WANGA"
...
Tsiku lina DAVIDE adakhala mkumalingalira za m'dalitso womwe anali nawo . Anakumbukila chinyamata chake momwe adaliri ndipo Mulungu anali atamutukula kuchoka ku ubusa wa ziweto ndikukhala mfumu.
Anawona nyumba yake ndipo adapenyanso nyumba ya Yehova ndipo adaganiza zomanga nyumba ya Yehova yapamwamba.
...
Adamuuza mneneri wa nthawiyo maganizo ake ndipo mneneri atawona kuti ganizolo linali labwino adamuuza David kuti apange zomwe ankaganizazo.
Usiku Mulungu adamuuza mneneri kuti akamuuze David asamange nyumbayo koma anzamange mwana wake .
...
Solomo mwana wa David adakwanilitsa lingaliro la bambo ake David.
Kachisi adamangidwa kwa zaka 40 koma sikunamveke kulira kwachipangizo chili chonse mpaka kachisi adamalizidwa kumanga.
Tsiku lomwe adasegulira kachisi uyu Solomo adamupempha Ambuye kuti adalitse malo komanso Kachisiyo ndipo adati;
"NGATI MUNTHU APEMPHERA POPENYA KUKACHITSIYO MULUNGU ADZIYANKHA PEMPHERO LAKE" (ndiyamika Ambuye kaachimenechi)
...
Yona adali mmimba mwa Mnsomba komanso m'madzi ndipo sankaona kunja koma adapempha mopenya kukachisiyo ndipo Mulungu adamva pemphero lake. YONA 2:4. Kotelo ichi chidali chiphunzitso cha a Israel chomapemphera poyang'ana kukachisi .Funso mkukhala kodi YONA adaziwa bwanji kuti iye akupenya kukachisi popeza adali mkati mwa mnsomba komanso mkati mwa madzi? By faith he presented his prayer. (Mwachikhulupiliro adapempha ndipo adayankhidwa)
...
NKhani ndiyoti Chikhulupiliro sichiona komwe munthu akupenya kapena komwe akuyang'ana chifukwa chikhulupiliro chimapyola miyamba. Chikhulupiliro chimapangisa zosatheka nkutheka.
Tsopano kupembedza moyang'ana kumawa kudali kokwanila kwa iwo omwe adali kumadzulo koma kwa iwo omwe adali kummawa kwa kachisi ankapembedza mopenya kumadzulo chifukwa nkomwe kunali kachitsi tsopano, choncho sizimatengera kupenya ku mmawa kapena kumadzulo koma kupenya komwe kuli Kachisi wa Yehova.
...
Apapa mutha kuona kuti Choopya sanali kachisiyo koma Mulungu yemwe adali mu kachisiyo ndiye adali wopambana. Phindu palibe ngati Mulungu sangakhale mukachisiyo. MASALIMO 127, AKAPANDA KUIMANGA NYUMBA YEHOVA AKUIMANGA AIMANGA NDIPO IGWIRA NTCHITO CHABE
...
Ndiye tsono lero Mau a Mulungu akuti; Komatu Mulungu sakhala mnyumba zomangidwa ndi manja a wanthu, Koma thupi munandikonzera ine. Mulungu adachoka mu kachisi womangidwa ndi manja nadzakhala mu thupi lotchedwa Yesu. Choncho onse opemphera ayenera kupemphera mwachikhulupiro mopenya Yesu.
Ndichifukwa chake pa YOHANE 4 VS 21 - 23
"Ambuye adati nthawi idzafika pamene kupemphera sikudzachitikanso mu phili kapena ku Yerusalem koma kudzachitika mu mnzimu ndi choonadi.
...
Kutero m'bale ndiimfa yake tikukumbukira leroyi, titapenya kwaiye mwachikhukupiro tikhoza kutchira kunthenda zathu,,tikhoza kusiya ntchito zathu zoipa ndikukhululukiridwa zochimwa zathu.
Zisakupepukireni abale, kalero kunali zambiri zomwe anthu amasatila kut akhululukiridwe zochimwa koma lero anapeleka mwana wake obadwa yekha kutichosera zonse zoipa kut tipulumutsidwe..kulibenso dzina lina loposa dzina lakut Yesu, utakhulupira mwa dzina ili uzapulumuka uzakhululukilidwa, uzakalowa muufumu wakumwamba, chitilatu ukadali ndi moyo uli ndi mphamvu pakut zamawa sizidziwika..
0 comments