Nkhondo itafika povuta Wankulu wasilikali wina anatumiza asilikali 1000 kuti akagonjetse adani.
Mwasikali wonsewo anaphedwa 999 ndikutsala msikali mmodzi.
Wotsalayi atawona kuti zinthu zanthina anthawira Ku mphanga, ali kumphangaku anayamba kupemphera Kwa Mulungu.
"Ambuye Mulungu ndipemphani mundipulumutse kwa adani anga andizinga kufuna kuchotsa moyo wanga, mukandipulutsa ndidzakutamandani nthawi yonse Ya moyo wanga"
Patapita kanthawi anawona kangaude akuluka chisa chake pa nkhomo la Mphanga lija.
Kenako anayamba kunyozera nkumati, Bwanji Ambuye mwatumiza kangaudeyo, mmalo mutumiza Chimwala chachikulu kuti Chidzantchinge pa nkhomopo.
Nthawi yomweyo anamva Kuyankhula kwa adani aja omwe anali chapafupi ndi mphangalo mmodzi mwa adaniwo anaganiza zoponyako bomba Ku mphangako koma wankulu wasilika anawakaniza anati "Iwe ukuona kuti papita nthawi padzenjepo pasanalowe kanthu okufuna unguononga zida zankhondo tawona pali akangaude okhaokha tiyeni tisachedwe tikamusake kutsogoloku , Changuu !!!!."
Apo ntima wake unatsika pansi nkuyamba kulira kudandaulira Mulungu ponyozera nthandizo kapena kuti Chipulumuntso Chomwe anapereka.
_______
Tiyeni tiphunzirepo Kanthu.
______________________
Ndikutheka unamupempha Galimoto Mulungu wakupatsa njinga, iwe uchilandire ndikuvomereza Mulungu salakwitsa komanso amadziwa zakudza kutsogolo kwako.
Pali zambiri zomwe wankhala ukupempha zinthu zambiri pa moyo wako koma mwina sakupatsa momwe umafunira . Usadere nkhawa Mulungu akudziwa chomwe akupanga pa moyo wako ndipo Muzonse Muyamike iye.
Paja Malembo akuti "Muzonse Yamikani Ambuye"
Mulungu wanthu salakwitsa ali NATO nthawi yopanga zinthu, mwina kutheka kumankhala kuteteza moyo wako.
Ndi mau amenewa , Mulungu odziwa kudalitsa , Akudalitseni potengapo gawo pa Uthengawu ndikudalitsa tsiku lanu Linkhale lopambana lero ndi Masiku onse ndi nthawi zosantha Amen
0 comments