Panali Mai ndi mwana wawo wamwamuna , omwe anali amasiye bambo apanyumbapo anamwalira .
Mwanayu Amaphunzira school, Ndipo Maiwa amasamalira mwanayu ndicholinga apite patsogolo ndi school yake.
Zamavuto azachuma ayi ndithu zinthu zimawavuta moti zakudya maiwa amachita maganyu Olima m'minda ya anthu ena kuti tsiku limenero adye.
Tsiku lina anakalima munda wa nkulu wina, atamaliza kulimako nkuluyo anamuuza maiyo kuti ndalama mubwere pakatha 3days pakali pano alibe.
Maiyu nkhawa inamugwira kuti ndikadyanji nanga mwana akabwera Ku school adya chani.
Anayesa kumupempha zakudya nkuluyi koma anakanitsitsa.
Mai uja anapita kunyumba anapeza mwana wafika Ku Chokera Ku school ali pa nkhonde milomo itatuwiratu mai uja chisoni Chinamupeza kuti amuuza chani mwanayi .
Mwana uja atawaona mai ake anawathamangira ndikuwakumbatira ,ndikuwauza mama ndimakukondani bwanji mukuoneka okhumudwa lero, mai aja anamufotokozera mwanayi momwe anayendera kuganyu kuja .
Mwanayi anamva Chisoni kuona mai ake akudandaula ndipo anawalimbitsa ntima musandaule nkhalani apa ndikuuzeni ka nkhani.
Atakhala pansi Mwana uja anayamba kuwafusa mafuso mai ake , fuso loyamba anawafusa Kuti, Kodi eti mami Mbalame sizilima? mai anayamba 'eya'
Iiiiiii ndetu Ku school kunabwera abusa amati ngati Mbalame sizilima kapena kufesa Kuli bwanji ife anthu oti Mulungu amatikonda , Amati tikasowa Chakudya , kaya Zovala ndi zina zosoweka pa Moyo wathu tizipemphera ndi Chinkhulupiliro, Mulungu Adzatipatsa. Mwana uja anawauza Choncho mai ake aja.
Kotero ali Chinkhalire Anagwirana manja ndikupemphera kwa Mulungu.
Patapita kampindi kochepa Neba wa maiwa anabwera kudzawalonjera , atalonjelana Neba wawo uja anayafusa kuti Masanawa ndimakuyang'anani kunabwera Nkulu wina akuti ndi M'bale wawo wa Malemu amuna anu anandisiyira Ndalama akuti muzithandikizira komanso mukhozetsere nyumbayi.
Mai awone ndalama MK 500,000 .
Anagwada pansi ndikuyangana kumwamba ndipo analira mokweza ndikuyamika Mulungu wa kumwamba pa Chachikulu chomwe wawachitira .
Moyo wawo unasintha ndipo anali kupemphera nthawi zonse komanso anayamba Business yomwe inachita bwino . Pano ndi anthu olozeka onse ankachitako maganyu amabwera kudzagwira Ganyu pa nkhomo lawo.
_______
Mulungu amasintha Nyengo
Mulungu wathu ndi Mulungu wazatheka bwanji . Tiyeni tizidalira pemphero pa masiku onse amoyo wathu. Mu pemphero muli Mzeru
Lilemekezeke Dzina la Yehova Mulungu wamwambamwamba Litamandike Dzina lake kuti Onse amitundu adziwe kuti iye Ndiye Kasupe wa Chikondi Chopanda Malire .
Wodala Iwo amva mau ake ndikuwatsatira
_________
Mulungu odziwa Kudalitsa Akudalitseni powerenga Uthengawu. Ndipo akuntchinjilizeni kumikwingwirima ya Dziko Lapansi.
___________
Amen
0 comments